Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 33:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo Esau anati, Zanga zikwanira; mbale wanga, khala nazo zako iwe wekha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo Esau anati, Zanga zindifikira; mbale wanga, khala nazo zako iwe wekha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Koma Esau adati, “Mbale wanga, zoŵeta zotere ndili nazo zambiri. Uli nazozi zikhale zako.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Koma Esau anati, “Mʼbale wanga, ine ndili nazo kale zambiri. Zinthu zakozi sunga.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 33:9
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Isaki atate wake anayankha nati kwa iye, Taona, pokhala pako mpa zonenepa za dziko lapansi, pa mame a kumwamba akudzera komwe.


Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako, nudzakhala kapolo wa mphwako. Ndipo padzakhala pamene udzapulumuka, udzachotsa goli lake pakhosi pako.


Ndipo Esau anamuda Yakobo chifukwa cha mdalitso umene atate wake anamdalitsa nao: ndipo Esau anati m'mtima mwake, Masiku a maliro a atate wanga ayandikira; pamenepo ndipo ndidzamupha mphwanga Yakobo.


Ndipo Yakobo anati, Iaitu, ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, mulandire mphatso yanga padzanja langa; pakuti popeza ndinaona nkhope yanu, monga anthu aona nkhope ya Mulungu, ndipo inu mwandivomereza ine.


Yehova ndipo anati kwa Kaini, Ali kuti Abele mphwako? Ndipo anati, Sindidziwai: kodi ndine woyang'anira mphwanga?


Njira za munthu zikakonda Yehova ayanjanitsana naye ngakhale adani ake.


Msundu uli ndi ana aakazi awiri ati, Patsa, patsa. Pali zinthu zitatu sizikhuta konse, ngakhale zinai sizinena, Kwatha:


Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu.


Ndipo pamene anazimva, analemekeza Mulungu; nati kwa iye, Uona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupirira; ndipo ali nacho changu onsewa, cha pa chilamulo;


Ndipo anachoka Ananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani panjira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.


osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m'thupi, ndiponso mwa Ambuye.


Pakuti ndinali nacho chimwemwe chambiri ndi chisangalatso pa chikondi chako, popeza mitima ya oyera mtima yatsitsimuka mwa iwe, mbale.


Ndipo ana a Israele anakwera nalira misozi pamaso pa Yehova mpaka madzulo; nafunsira kwa Yehova ndi kuti, Ndiyandikizenso kodi kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga? Ndipo Yehova anati, Mumkwerere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa