Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 33:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo Yakobo anati, Iaitu, ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, mulandire mphatso yanga padzanja langa; pakuti popeza ndinaona nkhope yanu, monga anthu aona nkhope ya Mulungu, ndipo inu mwandivomereza ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo Yakobo anati, Iaitu, ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, mulandire mphatso yanga pa dzanja langa; pakuti popeza ndinaona nkhope yanu, monga anthu aona nkhope ya Mulungu, ndipo inu mwandivomereza ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Yakobe adati, “Ai chonde, ngati mwandikomera mtima, landirani mphatso yanga. Ine ndikamaona nkhope yanu, ndiye ngati ndaona nkhope ya Mulungu, poti mwandilandira chonchi ndi manja aŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Yakobo anati, “Chonde musatero. Ngati mwandikomera mtima, landirani mphatso yangayi kuchokera kwa ine. Pakuti ndi mmene mwandirandira bwinomu, ine ndikamaona nkhope yanu ndikuchita ngati ndikuona nkhope ya Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 33:10
19 Mawu Ofanana  

taonanitu, kapolo wanu anapeza ufulu pamaso panu, ndipo munakuza chifundo chanu, chimene munandichitira ine, pakupulumutsa moyo wanga; ine sindikhoza kuthawira kuphiri kuti chingandipeze ine choipacho ndingafe;


Ndipo Yakobo anatcha dzina la malo amenewo, Penuwele: chifukwa ndaonana ndi Mulungu nkhope ndi nkhope, ndipo wapulumuka moyo wanga.


Landiranitu mdalitso wanga umene wafika kwa inu, pakuti Mulungu wandichitira ine zaufulu, ndipo zanganso zindikwanira. Ndipo anamkakamiza, nalandira.


Ndipo Esau anati, Zanga zikwanira; mbale wanga, khala nazo zako iwe wekha.


Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mau kuti, simudzaonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko.


Ndipo nthawi inayandikira kuti Israele adzafa, ndipo anaitana Yosefe mwana wake wamwamuna, nati kwa iye, Ngati ndapeza ufulu pamaso pako, ikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga, nundichitire ine zabwino ndi zoona: usandiikatu ine mu Ejipito;


Atapita masiku akumlira iye, Yosefe anati kwa mbumba ya Farao, kuti, Ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, nenanitu m'makutu a Farao kuti,


Ndipo mfumu inati, Apatukire kunyumba ya iye yekha, koma asaone nkhope yanga. Chomwecho Abisalomu anapatukira kunyumba ya iye yekha, wosaona nkhope ya mfumu.


Ndipo Abisalomu anakhala ku Yerusalemu zaka ziwiri zathunthu, osaona nkhope ya mfumu.


Abisalomu nayankha Yowabu, Ona, ndinatumiza kwa iwe kuti, Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukanena, Ine ndinabwereranji kuchokera ku Gesuri? Mwenzi nditakhala komweko; chifukwa chake tsono mundilole kuona nkhope ya mfumu; ndipo ngati mulinso mphulupulu mwa ine andiphe ndithu.


Nati iye, Chabwino, ndidzapangana nawe; koma ndikuikira chinthu chimodzi, ndicho kuti, sudzaona nkhope yanga, koma utsogole wabwera naye Mikala mwana wamkazi wa Saulo, pamene ubwera kudzaona nkhope yanga.


Apembedza Mulungu, ndipo amkomera mtima; m'mwemo aona nkhope yake mokondwera; ndipo ambwezera munthu chilungamo chake.


Umo ndidziwa kuti mukondwera ndi ine, popeza mdani wanga sandiseka.


Atero Yehova, Anthu opulumuka m'lupanga anapeza chisomo m'chipululu; Israele, muja anakapuma.


Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.


nadzaona nkhope yake; ndipo dzina lake lidzakhala pamphumi pao.


Potero anagwa nkhope yake pansi, nadziweramira pansi, nanena naye, Mwandikomera mtima chifukwa ninji kuti mundisamalira ine, popeza ndine mlendo?


Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa