Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 33:11 - Buku Lopatulika

11 Landiranitu mdalitso wanga umene wafika kwa inu, pakuti Mulungu wandichitira ine zaufulu, ndipo zanganso zindikwanira. Ndipo anamkakamiza, nalandira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Landiranitu mdalitso wanga umene wafika kwa inu, pakuti Mulungu wandichitira ine zaufulu, ndipo zanganso zindifikira. Ndipo anamkakamiza, nalandira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Chonde landirani mphatso ndakutengeraniyi. Mulungu adandikomera mtima, ndipo adandipatsa zosoŵa zanga zonse.” Adapitirira kumuumiriza, mpaka Esau adalandira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Chonde, landirani mphatso imene ndakutengeraniyi, popeza Mulungu wandikomera mtima kwambiri moti ndili ndi zonse zimene ndizifuna.” Ndipo popeza kuti Yakobo anamuwumiriza, Esau analandira.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 33:11
21 Mawu Ofanana  

Munthuyo ndipo analemera kwambiri, nali nazo zoweta zambiri, ndi akapolo aamuna ndi aakazi, ndi ngamira, ndi abulu.


Momwemo naolotsa mphatso patsogolo pake: ndipo iye yekha anagona usiku womwewo pachigono.


Ndipo Yakobo anati, Iaitu, ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, mulandire mphatso yanga padzanja langa; pakuti popeza ndinaona nkhope yanu, monga anthu aona nkhope ya Mulungu, ndipo inu mwandivomereza ine.


Ndipo Esau anati, Tiyeni timuke; nditsogolera ndine.


Ndipo Esau anati, Zanga zikwanira; mbale wanga, khala nazo zako iwe wekha.


Koma anamuumiriza kufikira anachita manyazi; pamenepo anati, Tumizani. Motero anatumiza amuna makumi asanu, namfunafuna iwo masiku atatu, osampeza.


Nati Naamani, Ulole ulandire matalente awiri. Namkakamiza namanga matalente awiri a siliva m'matumba awiri, ndi zovala zosintha ziwiri, nasenzetsa anyamata ake awiri; iwo anatsogola atazisenza.


Ndipo mbuye ananena kwa kapoloyo, Tuluka, nupite kumiseu ndi njira za kuminda, nuwaumirize anthu alowe, kuti nyumba yanga idzale.


Chifukwa chake palibe mmodzi adzitamande mwa anthu. Pakuti zinthu zonse nzanu;


monga akumva chisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga okhala opanda kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.


Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.


pakuti chizolowezi cha thupi chipindula pang'ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la kumoyo uno, ndi la moyo ulinkudza.


Nati iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwera, ndipatseninso zitsime za madzi. Pamenepo anampatsa zitsime za kumtunda, ndi zitsime za kunsi.


Ndipo anati kwa iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwera, ndipatsenso zitsime za madzi. Pamenepo Kalebe anampatsa zitsime za kumtunda ndi zitsime za kunsi.


Ndipo mphatso iyi mdzakazi wanu ndatengera mbuye wanga, ipatsidwe kwa anyamata akutsata mbuye wanga.


Ndipo pamene Davide anafika ku Zikilagi, anatumizako za zofunkhazo kwa akulu a Yuda, ndiwo abwenzi ake, nati, Siyi mphatso yanu ya zofunkha za adani a Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa