Genesis 33:13 - Buku Lopatulika13 Ndipo anati kwa iye, Mbuyanga adziwa kuti ana ali anthete, ndipo nkhosa ndi zoweta ndili nazo zilinkuyamwitsa: ndipo akathamangitsa tsiku limodzi zoweta zonse zidzafa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Ndipo anati kwa iye, Mbuyanga adziwa kuti ana ali ambowa, ndipo nkhosa ndi zoweta ndili nazo zilinkuyamwitsa: ndipo akathamangitsa tsiku limodzi zoweta zonse zidzafa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Tsono Yakobe adati, “Mbuyanga, mukudziŵa kuti anaŵa atopa, ndipo ndiyenera kusamalanso nkhosa ndi ng'ombe zimene zili ndi tiana. Ndikazikusa mofulumira kwambiri, ngakhale tsiku limodzi lokha, zifa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Koma Yakobo anati kwa iye, “Mbuye wanga, inu mudziwa kuti anawa ndi a nthete ndiponso ndiyenera kusamalira nkhosa ndi ngʼombe zimene zikuyamwitsa ana awo. Ngati ndizimenya kuti zifulumire, tsiku limodzi lokha nyamazo zidzafa. Onani mutuwo |