Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 33:14 - Buku Lopatulika

14 Mbuyanga atsogoleretu kapolo wake, ndipo ine ndidzazitsogolera pang'onopang'ono monga mwa mayendedwe a zoweta zili pamaso panga, ndi monga mwa mayendedwe a ana, mpaka ndifike kwa mbuyanga ku Seiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Mbuyanga atsogoleretu kapolo wake, ndipo ine ndidzazitsogolera pang'onopang'ono monga mwa mayendedwe a zoweta zili pamaso panga, ndi monga mwa mayendedwe a ana, mpaka ndifike kwa mbuyanga ku Seiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Chonde mbuyanga, tsogolaniko, ine ndiziyenda pang'onopang'ono pambuyo pa zoŵeta ndi ana anga, mpaka ndikakupezani ku Seiri.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Choncho, mbuye wanga lolani kuti mutsogole. Ine ndiziyenda pangʼonopangʼono pambuyo pa ziwetozi ndi anawa mpaka ndikafika ku Seiri.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 33:14
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anatumiza amithenga patsogolo pake kwa Esau mkulu wake, ku dziko la Seiri, kudera la ku Edomu.


Ndipo anauza iwo kuti, Mukanene chotere kwa mbuyanga Esau: Atero Yakobo kapolo wako, ndakhala pamodzi naye Labani, ndipo ndakhalabe kufikira tsopano lino:


Ndipo anati kwa iye, Mbuyanga adziwa kuti ana ali anthete, ndipo nkhosa ndi zoweta ndili nazo zilinkuyamwitsa: ndipo akathamangitsa tsiku limodzi zoweta zonse zidzafa.


Ndipo tsopano, taonani ana a Amoni, ndi Mowabu, ndi a kuphiri la Seiri, amene simunalole Israele awalowere, pakutuluka iwo m'dziko la Ejipito, koma anawapatukira osawaononga;


Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.


Atero Ambuye Yehova, Popeza Mowabu ndi Seiri akuti, Taona nyumba ya Yuda ikunga amitundu onse;


Ndipo ndi mafanizo otere ambiri analankhula nao mau, monga anakhoza kumva;


Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.


Ndinadyetsa inu mkaka, si chakudya cholimba ai; pakuti simungachithe; ngakhale tsopano lino simungachithe; pakuti mulinso athupi;


Pamenepo tinabwerera, ndi kuyenda kunka kuchipululu, kutsata njira ya Nyanja Yofiira, monga Yehova adanena ndi ine; ndipo tinapaza phiri la Seiri masiku ambiri.


Yehova, muja mudatuluka mu Seiri, muja mudayenda kuchokera ku thengo la Edomu, dziko linanjenjemera, thambo lomwe linakha, inde mitambo inakha madzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa