Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 30:6 - Buku Lopatulika

6 Rakele ndipo anati, Mulungu wandiweruzira ine, namva mau anga, nandipatsa ine mwana; chifukwa chake anamutcha dzina lake Dani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Rakele ndipo anati, Mulungu wandiweruzira ine, namva mau anga, nandipatsa ine mwana; chifukwa chake anamutcha dzina lake Dani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tsono Rakele adati, “Mulungu waweruza mondikomera mtima. Wamva pemphero langa, ndipo wandipatsa mwana wamwamuna.” Motero mwanayo adamutcha Dani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Pamenepo Rakele anati, “Mulungu waweruza mondikomera mtima, wamva kupempha kwanga ndipo wandipatsa mwana wa mwamuna.” Choncho anamutcha Dani.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 30:6
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Biliha anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna.


Ndipo Biliha mdzakazi wake wa Rakele anatenganso pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachiwiri.


ana aamuna a Biliha mdzakazi wake wa Rakele: ndiwo Dani ndi Nafutali;


Ndi ana aamuna a Dani: Husimu.


Mundiweruze monga mwa chilungamo chanu, Yehova Mulungu wanga; ndipo asandisekerere ine.


Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo. Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.


Ndipo ndinagula mpango monga mwa mau a Yehova, ndi kuvala m'chuuno mwanga.


Chifukwa chake ndidzabalalitsa iwo, monga ziputu zakupita, ndi mphepo ya kuchipululu.


Yehova, mwaona choipa anandichitiracho, mundiweruzire.


A ana a Dani, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;


Naimirire awa paphiri la Ebala, kutemberera: Rubeni, Gadi, ndi Asere, ndi Zebuloni, Dani ndi Nafutali.


Ndi za Dani anati, Dani ndiye mwana wa mkango, wakutumpha motuluka mu Basani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa