Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 30:32 - Buku Lopatulika

32 Ndidzapita ine lero pakati pa ziweto zonse kusankhasankha m'menemo zoweta zonse zamathothomathotho ndi zamawangamawanga, ndi za nkhosa zonse, ndi mbuzi zonse zamawangamawanga ndi zamathothomathotho: zotero zidzakhala malipiro anga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Ndidzapita ine lero pakati pa ziweto zonse kusankhasankha m'menemo zoweta zonse zamathothomathotho ndi zamawangamawanga, ndi za nkhosa zonse, ndi mbuzi zonse zamawangamawanga ndi zamathothomathotho: zotero zidzakhala malipiro anga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Lero ndipita pakati pa zoŵeta zanu zonse. Ndipatula nkhosa zonse zakuda, ndiponso mbuzi zonse zamaŵangamaŵanga ndi zamathothomathotho. Malipiro amene ndifuna ine ndi ameneŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Mundilole ndiyendeyende pakati pa ziweto zanu lero ndi kuchotsamo mwana wankhosa wamkazi aliyense wakuda, mbuzi iliyonse yamathothomathotho ndi yamawangamawanga. Zimenezi ndiye zikhale malipiro anga.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 30:32
5 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anati, Ndikupatsa iwe bwanji? Ndipo Yakobo anati, Usandipatse ine kanthu; ukandichitira ine chotero, ine ndidzadyetsanso ndi kusunganso ziweto zako.


Chotero chilungamo changa chidzandivomereza m'tsogolo pamene udzandifika chifukwa cha malipiro amene ali patsogolo pako: iliyonse yosakhala yamathothomathotho ndi yamawangamawanga ya mbuzi, ndi iliyonse ya nkhosa yosakhala yakuda, ikapezedwa ndi ine, udzaiyesa yakuba.


Tsiku lomwelo Labani anachotsa atonde amene anali amipyololomipyololo ndi amathothomathotho, ndi mbuzi zazikazi zinali zamawangamawanga ndi zamathothomathotho zonse zinali zoyera pang'ono, ndi zakuda zonse za nkhosa, napatsa m'dzanja la ana ake aamuna.


Ndipo panali potenga mabere ziwetozo, ine ndinatukula maso anga, ndipo ndinapenya m'kulota, taonani, atonde okwera ziweto anali amipyololomipyololo, amathothomathotho, ndi amawangamawanga.


Akati chotero, Zamathothomathotho zidzakhala malipiro ako, zoweta zonse zinabala zamathothomathotho; ndipo akati iye chotere, Zamipyololomipyololo zidzakhala malipiro ako, ziweto zonse zinabala mipyololomipyololo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa