Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 30:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo Leya anati, Mulungu anandipatsa ine mphatso yabwino; tsopano mwamuna wanga adzakhala ndi ine, chifukwa ndambalira iye ana aamuna asanu ndi mmodzi; ndipo anamutcha dzina lake Zebuloni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo Leya anati, Mulungu anandipatsa ine mphatso yabwino; tsopano mwamuna wanga adzakhala ndi ine, chifukwa ndambalira iye ana amuna asanu ndi mmodzi; ndipo anamutcha dzina lake Zebuloni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Ndipo adati, “Mulungu wandipatsa mphotho yokoma. Tsopano mwamuna wanga adzakhala nane chifukwa ndamubalira ana aamuna asanu ndi mmodzi.” Motero mwanayo adamutcha Zebuloni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Pamenepo Leya anati, “Mulungu wandipatsa mphatso yapamwamba. Tsopano mwamuna wanga adzandilemekeza chifukwa ndamubalira ana aamuna asanu ndi mmodzi.” Choncho anamutcha Zebuloni.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 30:20
15 Mawu Ofanana  

Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna, nati, Tsopano lino mwamuna wanga adzadziphatika kwa ine chifukwa ndambalira iye ana aamuna atatu; chifukwa chake anamutcha dzina lake Levi.


Ndipo iye anati kwa Rakele, Kodi mpachabe kuti iwe wachotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kuchotsanso mankhwala a mwana wanga? Rakele ndipo anati, Chifukwa chake iye adzagona nawe usiku uno chifukwa cha mankhwala a mwana wako.


Ndipo Leya anatenganso pakati nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachisanu ndi chimodzi.


Pambuyo pake ndipo anabala mwana wamkazi, namutcha dzina lake Dina.


Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga.


ana aamuna a Leya: ndiwo Rubeni mwana woyamba wa Yakobo, ndi Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Zebuloni, ndi Isakara;


Ndi ana aamuna a Zebuloni: Seredi, ndi Eloni ndi Yaleele.


Zebuloni adzakhala m'mphepete mwa nyanja; ndipo iye adzakhala dooko la ngalawa; ndipo malire ake adakhala pa Sidoni.


Apo pali Benjamini wamng'ono, wakuwachita ufumu, akulu a Yuda, ndi a upo wao, akulu a Zebuloni, akulu a Nafutali.


Atate wake akakana konse kumpatsa iye, alipe ndalama monga mwa cholipa cha anamwali.


ndipo anachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye mu Kapernao wa pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafutali:


Naimirire awa paphiri la Ebala, kutemberera: Rubeni, Gadi, ndi Asere, ndi Zebuloni, Dani ndi Nafutali.


Ndipo Baraki anaitana Zebuloni ndi Nafutali asonkhane ku Kedesi; iye nakwera ndi anthu zikwi khumi akumtsata; Deboranso anakwera kunka naye.


Anafika Aefuremu amene adika mizu mu Amaleke; Benjamini anakutsata iwe pakati pa anthu ako. Ku Makiri kudachokera olamulira, ndi ku Zebuloni iwo akutenga ndodo ya mtsogoleri.


Nati Saulo, Mudzatero kwa Davide, kuti mfumu safuna cholowolera china, koma nsonga za makungu zana limodzi za Afilisti, kuti abwezere chilango adani a mfumu. Koma Saulo anaganizira kupha Davide ndi dzanja la Afilisti.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa