Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 30:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo Rubeni ananka masiku akudula tirigu, napeza zipatso za mankhwala a chikondi m'thengo, nazitengera kwa amake Leya. Ndipo Rakele anati kwa Leya, Undipatseko mankhwala a mwana wako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo Rubeni ananka masiku akudula tirigu, napeza zipatso za mankhwala a chikondi m'thengo, nazitengera kwa amake Leya. Ndipo Rakele anati kwa Leya, Undipatseko mankhwala a mwana wako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Pa nthaŵi yodula tirigu, Rubeni adapita ku minda, nakapezako zipatso za mankhwala a chisulo, ndipo adadzapatsa Leya mai wake. Rakele adauza Leya kuti, “Chonde patseko mankhwala amene mwana wako wakufuniraŵa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Pa nthawi yokolola tirigu, Rubeni anapita ku munda ndipo anapezako zipatso za mankhwala wobereketsa. Tsono anatengerako mayi wake Leya. Rakele anati kwa Leya, “Chonde patseko mankhwala wakupezera mwana wakowo.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 30:14
5 Mawu Ofanana  

ndipo Esau anati kwa Yakobo, Undipatse ndidye chofiiracho; chifukwa ndalefuka: chifukwa chake anamutcha dzina lake Edomu.


Ndipo iye anati kwa Rakele, Kodi mpachabe kuti iwe wachotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kuchotsanso mankhwala a mwana wanga? Rakele ndipo anati, Chifukwa chake iye adzagona nawe usiku uno chifukwa cha mankhwala a mwana wako.


Ndipo Yakobo anadza madzulo kuchokera kumunda, ndipo Leya ananka kukomana naye, nati, Ulowe kwa ine chifukwa ndakulipilira iwe ndi mankhwala a mwana wanga. Ndipo anagona naye usiku womwewo.


Mankhwala a chikondi anunkhira, ndi pamakomo pathu zipatso zabwino, za mitundumitundu, zakale ndi zatsopano, zimene ndakukundikira iwe, wokondedwa wanga.


Ndi kumalire a Simeoni kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Isakara, limodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa