Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 30:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo Leya anati, Ndakondwa ine! Chifukwa kuti ana aakazi adzanditcha ine wokondwa: ndipo anamutcha dzina lake Asere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo Leya anati, Ndakondwa ine! Chifukwa kuti ana akazi adzanditcha ine wokondwa: ndipo anamutcha dzina lake Asere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Apo Leya adati, “Ndakondwa! Ndipo akazi adzanditchula wamwai.” Motero mwanayo adamutcha Asere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Pamenepo Leya anati, “Ndakondwa bwanji! Amayi adzanditcha ine wokondwa.” Choncho anamutcha Aseri.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 30:13
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Zilipa mdzakazi wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna wachiwiri.


ndipo ana aamuna a Zilipa mdzakazi wake wa Leya: ndiwo Gadi ndi Asere: amenewo ndi ana aamuna a Yakobo amene anabala iye mu Padanaramu.


Ndi ana aamuna a Asere: Imina, ndi Isiva, ndi Isivi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao; ndi ana a Beriya: Hebere, ndi Malikiele.


Ndi Asere, chakudya chake ndicho mafuta, ndipo adzapereka zolongosoka zachifumu.


Anake adzanyamuka, nadzamutcha wodala; mwamuna wake namtama, nati,


Nkhunda yanga, wangwiro wangayu, ndiye mmodzi; ndiye wobadwa yekha wa amake; ndiye wosankhika wa wombala. Ana aakazi anamuona, namutcha wodala; ngakhale akazi aakulu a mfumu, ndi akazi aang'ono namtamanda.


chifukwa Iye anayang'anira umphawi wa mdzakazi wake; pakuti taonani, kuyambira tsopano, anthu a mibadwo yonse adzanditchula ine wodala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa