Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 30:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo iye anati kwa Rakele, Kodi mpachabe kuti iwe wachotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kuchotsanso mankhwala a mwana wanga? Rakele ndipo anati, Chifukwa chake iye adzagona nawe usiku uno chifukwa cha mankhwala a mwana wako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo iye anati kwa Rakele, Kodi mpachabe kuti iwe wachotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kuchotsanso mankhwala a mwana wanga? Rakele ndipo anati, Chifukwa chake iye adzagona nawe usiku uno chifukwa cha mankhwala a mwana wako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Leya adayankha kuti, “Kodi sunakhutitsidwebe ndi mwamuna wanga udandilandayu? Tsopano ufuna kutenganso mankhwala a chisulo amene mwana wanga wandifunira?” Rakele adati, “Ukandipatsa mankhwala a chisulo ochokera kwa mwana wakoŵa, ŵamunaŵa akhala ndi iwe usiku uno.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Koma iye anati kwa Rakele, “Kodi sizinakukwanire kulanda mwamuna wanga? Ukuti utengenso mankhwala a mwana wangawa.” Iye anati, “Chabwino, agone ndi iwe usiku uno kuti tisinthane ndi mankhwala a mwana wakowo.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 30:15
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Rubeni ananka masiku akudula tirigu, napeza zipatso za mankhwala a chikondi m'thengo, nazitengera kwa amake Leya. Ndipo Rakele anati kwa Leya, Undipatseko mankhwala a mwana wako.


Ndipo Yakobo anadza madzulo kuchokera kumunda, ndipo Leya ananka kukomana naye, nati, Ulowe kwa ine chifukwa ndakulipilira iwe ndi mankhwala a mwana wanga. Ndipo anagona naye usiku womwewo.


Ndipo iye anati, Mverani inu tsopano, inu a nyumba ya Davide; kodi ndi kanthu kakang'ono kwa inu kutopetsa anthu, kuti inu mutopetsa Mulungu wanga?


Koma sunayende m'njira zao, kapena kuchita monga mwa zonyansa zao pang'ono pokha; unawaposa iwo m'kuvunda kwako, m'njira zako zonse.


kodi ndi chinthu chaching'ono kuti watikweza kutichotsa m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, kutipha m'chipululu; koma udziyesanso ndithu kalonga wa ife?


Koma kwa ine kuli kanthu kakang'ono ndithu kuti ndiweruzidwe ndi inu, kapena pa bwalo la munthu; koma sindiweruza ngakhale ndekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa