Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 29:3 - Buku Lopatulika

3 Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa chitsime pamalo pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa chitsime pamalo pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Nkhosa zonsezo zitasonkhana pamodzi kumeneko, abusa oŵeta nkhosazo ndiwo ankachotsa mwalawo pachitsimepo, kuti nkhosa zaozo zimwe. Zitatha kumwako, ankakunkhunizanso mwalawo kutseka pachitsimepo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Amati nkhosa zonse zikasonkhana, abusawo ankagudubuza mwalawo, kuwuchotsa ndi kumwetsa madzi nkhosazo. Kenaka ankawubwezera mwalawo pamalo pake, pakamwa pa chitsimepo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 29:3
6 Mawu Ofanana  

Ndipo anayang'ana, taonani, chitsime m'dambo, ndipo, taonani, magulu atatu a nkhosa alinkugona kumeneko: pakuti pachitsimepo anamwetsa nkhosa; ndipo mwala wa pakamwa pa chitsime unali waukulu.


Ndipo anati Yakobo kwa iwo, Abale anga, ndinu a kuti inu? Nati, Ndife a ku Harani.


Ndipo anati, Sitingathe, koma zitasonkhana ziweto zonse, ndipo atagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime ndiko; pamenepo ndipo tizimwetsa nkhosa.


Pamenepo anadza abusa nawapirikitsa; koma Mose anauka nawathandiza, namwetsa gulu lao.


Mlongo wanga, mkwatibwi ndiye munda wotsekedwa; ngati kasupe wotsekedwa, ndi chitsime chopikiza.


Posamveka phokoso la amauta potunga madzi, pomwepo adzafotokozera zolungama anazichita Yehova, zolungama anazichita m'madera ake, mu Israele. Pamenepo anthu a Yehova anatsikira kuzipata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa