Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 29:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo anayang'ana, taonani, chitsime m'dambo, ndipo, taonani, magulu atatu a nkhosa alinkugona kumeneko: pakuti pachitsimepo anamwetsa nkhosa; ndipo mwala wa pakamwa pa chitsime unali waukulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo anayang'ana, taonani, chitsime m'dambo, ndipo, taonani, magulu atatu a nkhosa alinkugona kumeneko: pakuti pachitsimepo anamwetsa nkhosa; ndipo mwala wa pakamwa pa chitsime unali waukulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Atafikako adaona chitsime ku busa, ndiponso magulu atatu a nkhosa zitagona pambali pa chitsimecho. Nkhosazo zinkamwa m'chitsime chimenechi chomwe pamwamba pake panali mwala waukulu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Atafika kumeneko anaona chitsime ku busa ndipo panali magulu atatu a nkhosa zitagona pafupi ndi chitsimecho chifukwa nkhosazo zimamwetsedwa madzi ochokera mʼchitsimecho. Pamwamba pa chitsimecho panali mwala waukulu.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 29:2
12 Mawu Ofanana  

Ndipo mnyamatayo anatenga ngamira khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m'dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.


Ndipo anagwaditsa ngamira zake kunja kwa mzinda, ku chitsime cha madzi nthawi yamadzulo, nthawi yotuluka akazi kudzatunga madzi.


Taonani, ine ndiima pa chitsime cha madzi; ndipo ana aakazi a m'mzinda atuluka kudzatunga madzi;


Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa chitsime pamalo pake.


Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha.


Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuwa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawachitira chifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera.


koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira kumoyo wosatha.


ndipo pamenepo panali chitsime cha Yakobo. Ndipo Yesu, popeza analema ndi ulendo wake, motero anakhala pachitsime.


chifukwa Mwanawankhosa wakukhala pakati pa mpando wachifumu adzawaweta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pao.


Posamveka phokoso la amauta potunga madzi, pomwepo adzafotokozera zolungama anazichita Yehova, zolungama anazichita m'madera ake, mu Israele. Pamenepo anthu a Yehova anatsikira kuzipata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa