Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 29:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Yakobo ananka ulendo wake, nafika ku dziko la anthu a kum'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Yakobo ananka ulendo wake, nafika ku dziko la anthu a kum'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tsono Yakobe adapitirira ulendo wake, kupita ku dziko la anthu akuvuma.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yakobo anapitiriza ulendo wake kupita ku dziko la anthu a kummawa.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 29:1
17 Mawu Ofanana  

Ndipo mnyamatayo anatenga ngamira khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m'dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.


ndipo Isaki anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Mwaramu wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Mwaramu.


Koma kwa ana a akazi ake aang'ono amene Abrahamu anali nao Abrahamu anapatsa mphatso, nawachotsa iwo kwa Isaki mwana wake, akali ndi moyo, kuti anke kum'mawa, ku dziko la kum'mawa.


Ndipo Mulungu anati kwa Yakobo, Nyamuka nukwere kunka ku Betele nukhale kumeneko: numange kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anaonekera kwa iwe pamene unathawa ku nkhope ya Esau mbale wako.


Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, natcha pamenepo El Betele: pakuti kumeneko Mulungu anaonekera kwa iye muja anathawa pa nkhope ya mbale wake.


Ndipo nzeru ya Solomoni inaposa nzeru za anthu onse akum'mawa, ndi nzeru zonse za ku Ejipito.


Ndidzathamangira njira ya malamulo anu, mutakulitsa mtima wanga.


Ndinafulumira, osachedwa, kusamalira malamulo anu.


Tiye, idya zakudya zako mokondwa, numwe vinyo wako mosekera mtima; pakuti Mulungu wavomerezeratu zochita zako.


Ndipo Yakobo anathawira kuthengo la Aramu, ndi Israele anagwira ntchito chifukwa cha mkazi, ndi chifukwa cha mkazi anaweta nkhosa.


Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ku Aramu ananditenga Balaki, mfumu ya Mowabu ananditenga ku mapiri a kum'mawa, Idza, udzanditembererere Yakobo. Idza, nudzanyoze Israele.


Ndipo kunali, akabzala Israele, amakwera Amidiyani, ndi Amaleke, ndi ana a kum'mawa, inde amawakwerera;


Pamenepo Amidiyani onse ndi Aamaleke ndi ana a kum'mawa anasonkhana pamodzi naoloka, namanga misasa m'chigwa cha Yezireele.


Ndipo Amidiyani ndi Aamaleke ndi ana onse a kum'mawa ali gonere m'chigwa, kuchuluka kwao ngati dzombe; ndi ngamira zao zosawerengeka, kuchuluka kwao ngati mchenga wa m'mphepete mwa nyanja.


Zeba ndi Zalimuna ndipo anali mu Karikori, ndi a m'misasa ao pamodzi nao, amuna monga zikwi khumi ndi zisanu; ndiwo otsala onse a khamu lonse la ana a kum'mawa; popeza atagwa amuna zikwi zana limodzi ndi makumi awiri akusolola lupanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa