Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 27:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo panali atakalamba Isaki, ndi maso ake anali akhungu losaona nalo, anamuitana Esau mwana wake wamwamuna wamkulu, nati kwa iye, Mwana wanga; ndipo anati kwa iye, Ndine pano.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo panali atakalamba Isaki, ndi maso ake anali akhungu losaona nalo, anamuitana Esau mwana wake wamwamuna wamkulu, nati kwa iye, Mwana wanga; ndipo anati kwa iye, Ndine pano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Isaki atakalamba, adachita khungu, mwakuti sankatha kupenya. Tsono adatumiza mau kuti Esau mwana wake wamkulu abwere. Atabwera, Isaki adamuitana kuti, “Mwana wanga!” Iye adavomera kuti, “Ŵaŵa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Isake atakalamba maso ake anachita khungu mwakuti sankatha kuona. Iye anayitana mwana wake wamkulu Esau nati kwa iye, “Mwana wanga.” Iye anayankha, “Ine abambo.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 27:1
8 Mawu Ofanana  

Ndipo anati Yakobo, Undilumbirire ine lero lomwe, ndipo analumbirira iye; nagulana ndi Yakobo ukulu wake.


Koma maso a Israele anali akhungu mu ukalamba wake, ndipo sanathei kuona. Ndipo anadza nao pafupi; ndipo anapsompsona iwo, nawafungatira.


Natero mkazi wa Yerobowamu, nanyamuka nanka ku Silo, nalowa m'nyumba ya Ahiya. Koma Ahiya sanathe kupenya, popeza maso ake anali tong'o, chifukwa cha ukalamba wake.


tsikulo omwe asunga nyumba adzanthunthumira, amuna olimba nadzawerama, akupera nadzaleka poperewera, omwe ayang'ana pamazenera nadzadetsedwa;


Yesu anayankha, Sanachimwe ameneyo, kapena atate wake ndi amake; koma kuti ntchito za Mulungu zikaonetsedwe mwa iye.


Ndipo zaka zake za Mose ndizo zana limodzi ndi makumi awiri, pakumwalira iye; diso lake silinachite mdima, ndi mphamvu yake siidaleke.


Ndipo kunali nthawi yomweyo Eli atagona m'malo mwake (maso ake anayamba chizirezire osatha kupenya bwino);


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa