Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 26:33 - Buku Lopatulika

33 Ndipo anatcha dzina lake Siba, chifukwa chake dzina la mzindawo ndi Beereseba kufikira lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Ndipo anatcha dzina lake Siba, chifukwa chake dzina la mudziwo ndi Beereseba kufikira lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Isaki adachitcha Siba. Nchifukwa chake mzindawo umatchedwa Beereseba mpaka lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Iye chitsimecho anachitcha Pangano. Nʼchifukwa chake mzindawu umatchedwa Beeriseba mpaka lero.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 26:33
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.


Chifukwa chake anatcha malowo Beereseba: chifukwa pamenepo analumbira onse awiri.


Ndipo iwo anati, Kuona tinaona kuti Yehova ali ndi iwe; ndipo tinati, Tilumbiriranetu tonse awiri, ife ndi iwe, tichite pangano ndi iwe;


Ndipo panali tsiku lomwelo anyamata ake a Isaki anadza namuuza iye za chitsime chimene anakumba, nati kwa iye, Tapeza madzi.


ndi mu Hazara-Suwala, ndi mu Beereseba ndi midzi yake,


koma musamafuna Betele, kapena kumalowa mu Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Betele adzasanduka chabe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa