Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 24:29 - Buku Lopatulika

29 Ndipo Rebeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani; ndipo Labani anathamangira munthuyo kunja ku kasupe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Ndipo Rebeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani; ndipo Labani anathamangira munthuyo kunja ku kasupe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Apo Labani, mlongo wa Rebekayo, adaonadi chipini chija pamodzi ndi zigwinjiri pa mikono ya mlongo wakeyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Tsono Rebeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 24:29
8 Mawu Ofanana  

Ndipo panali, pamene anaona mphete ndi zingwinjiri pa manja a mlongo wake, pamene anamva mau a Rebeka mlongo wake, akuti, Chotero ananena ndi ine munthuyo; Labani anafika pa munthuyo; taonani, anaimirira pa ngamira pakasupe.


Ndipo mlongo wake ndi amake anati, Namwali akhale ndi ife masiku akuwerengeka, afikire khumi; patsogolo pake iye adzamuka.


Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse chipata cha iwo akudana nao.


ndipo Isaki anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Mwaramu wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Mwaramu.


Ndipo tsopano mwana wanga, tamvera mau anga: tauka, nuthawire kwa Labani mlongo wanga ku Harani;


Tauka, nupite ku Padanaramu, kunyumba ya Betuele, atate wa amai ako; ukadzitengere mkazi wa kumeneko kwa ana aakazi a Labani mlongo wake wa amai ako.


Ndipo panali pamene Labani anamva mbiri ya Yakobo mwana wa mlongo wake, iye anathamangira kukakomana naye namfungatira, nampsompsona, namlowetsa m'nyumba mwake. Ndipo iye anamfotokozera Labani zinthu zonsezo.


Ndipo anati kwa iwo, Kodi mumdziwa Labani mwana wake wa Nahori? Nati, Timdziwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa