Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 24:30 - Buku Lopatulika

30 Ndipo panali, pamene anaona mphete ndi zingwinjiri pa manja a mlongo wake, pamene anamva mau a Rebeka mlongo wake, akuti, Chotero ananena ndi ine munthuyo; Labani anafika pa munthuyo; taonani, anaimirira pa ngamira pakasupe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Ndipo panali, pamene anaona mphete ndi zingwinjiri pa manja a mlongo wake, pamene anamva mau a Rebeka mlongo wake, akuti, Chotero ananena ndi ine munthuyo; Labani anafika pa munthuyo; taonani, anaimirira pa ngamira pakasupe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Atamva mlongo wake akusimba zimene munthu uja adaamuuza, Labaniyo adathamangira kuchitsime kumene kunali munthuko. Adakafika pamalo pomwe adaaima wantchito wa Abrahamu, pafupi ndi ngamira zija kuchitsimeko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Iyeyu atangoona chipini pa mphuno ndi zibangiri pa mikono ya mlongo wake komanso kumva zimene mlendo uja ananena kwa Rebekayo, anathamangira kwa mlendo uja, ndipo anamupeza atangoyima ndi ngamira zake pafupi ndi chitsime.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 24:30
7 Mawu Ofanana  

Ndipo panali zitatha kumwa ngamira, munthuyo anatenga mphete yagolide ya kulemera kwake sekeli latheka, ndi zingwinjiri ziwiri za m'manja ake, kulemera kwake masekeli khumi a golide.


Ndipo Rebeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani; ndipo Labani anathamangira munthuyo kunja ku kasupe.


Ndipo anati, Talowa iwe, wodalitsidwa ndi Yehova; uimiriranji kunjako? Chifukwa kuti ndakonzeratu nyumba, ndi malo a ngamira.


mbera, ndi makoza, ndi nsalu za pankhope;


Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zake, kapena mkwatibwi zovala zake? Koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka.


Ndipo phokoso lalikulu lidaleka pomwepo, ndipo pamodzi ndi anthu wamba anabwera nao olodzera ochokera kuchipululu, naika makoza m'manja mwa awiriwo, ndi akorona okongola pamitu pao.


Ndipo iye anati kwa amai wake, Ndalama zija mazana khumi ndi limodzi anakuberani zimene munatembererapo, ndi kunenanso m'makutu mwanga, taonani ndalamazo ndili nazo, ndinazitenga ndine. Pamenepo amai wake anati, Yehova adalitse mwana wanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa