Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 18:32 - Buku Lopatulika

32 Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwa khumi m'menemo? Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha khumi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwa khumi m'menemo? Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha khumi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Abrahamu adati, “Chonde, musandikwiyire Ambuye, koma ndilankhule kamodzi kokhaka. Nanga mutapezeka khumi okha?” Aponso Chauta adati, “Ndikapeza olungama khumi, sindidzauwononga mzindawo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Kenaka Abrahamu anati, “Pepani Ambuye musandipsere mtima, ndingoyankhula kamodzi kokhaka basi. Bwanji atangopezeka khumi okha mʼmenemo?” Iye anayankha nati, “Chifukwa cha khumiwo, sindidzawuwononga.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 18:32
21 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m'menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m'menemo sindidzachita.


Ndipo anati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye: kapena akapezedwa makumi awiri m'menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi awiri.


Ndipo Yuda anayandikira kwa iye nati, Mfumu, kapolo wanu aneneretu m'makutu a mbuyanga, mtima wanu usapse pokwiya ndi kapolo wanu; chifukwa muli ngati Farao.


Akakhala kwa iye mthenga, womasulira mau mmodzi mwa chikwi, kuonetsera munthu chomuyenera;


Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.


Ndipo Yehova analeka choipa adanenachi, kuwachitira anthu ake.


Nsembe ya oipa inyansa Yehova; koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa.


Atero Yehova, Monga vinyo watsopano apezedwa m'tsango, ndipo wina ati, Usaliononge, pakuti muli mdalitso m'menemo, ndidzachita chifukwa cha atumiki anga, kuti ndisawaononge onse.


Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ake, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakuchita zolungama, wakufuna choonadi; ndipo ndidzamkhululukira.


Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.


Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;


Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,


Ndipo Gideoni ananena ndi Mulungu, Mkwiyo wanu usandiyakire, ndinene kamodzi kokha: ndikuyeseni kamodzi kokha ndi chikopa; paume pachikopa pokha, ndi panthaka ponse pakhale mame.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa