Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 18:31 - Buku Lopatulika

31 Ndipo anati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye: kapena akapezedwa makumi awiri m'menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Ndipo anati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye: kapena akapezedwa makumi awiri m'menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Tsono Abrahamu adati, “Ndapota nanu, khululukireni kulimba mtima chotere polankhula ndi Inu Ambuye. Nanga mutapezeka olungama 20?” Chauta adati, “Ndikapeza anthu olungama 20, sindidzauwononga mzindawo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Abrahamu anati, “Tsono poti ndalimba mtima chonchi kumayankhula ndi Ambuye, bwanji atangopezeka anthu makumi awiri okha?” Iye anati, “Chifukwa cha anthu makumi awiriwo, sindidzawuwononga.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 18:31
10 Mawu Ofanana  

Ndipo anayankha Abrahamu nati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine fumbi ndi phulusa:


Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m'menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m'menemo sindidzachita.


Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwa khumi m'menemo? Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha khumi.


Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye?


Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;


Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa, chifukwa ali bwenzi lake, koma chifukwa cha liuma lake adzauka nadzampatsa iye zilizonse azisowa.


Ndipo anawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafooka mtima;


mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,


Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa