Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 18:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo Abrahamu anayandikira nati, Kodi mudzaononga olungama pamodzi ndi oipa?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo Abrahamu anayandikira nati, Kodi mudzaononga olungama pamodzi ndi oipa?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Apo Abrahamu adayandikira kwa Chauta namufunsa kuti, “Kodi monga mudzaonongadi anthu osachimwa pamodzi ndi ochimwa?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Kenaka Abrahamu anasendera kufupi ndi Iye nati, “Kodi mudzawonongera kumodzi wolungama ndi woyipa?

Onani mutuwo Koperani




Genesis 18:23
15 Mawu Ofanana  

Kapena alipo olungama makumi asanu m'kati mwa mzinda; kodi mudzaononga, simudzasiya malowo chifukwa cha olungama makumi asanu ali momwemo?


Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?


Koma Abimeleki sanayandikire naye; ndipo anati, Ambuye, kodi mudzaphanso mtundu wolungama?


Ndipo Davide analankhula ndi Yehova pamene anaona mthenga wakudwalitsa anthu, nati, Onani ndachimwa ine, ndinachita mwamphulupulu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu likhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga.


Kodi munthu woipidwa nacho chiweruzo adzalamulira? Ndipo kodi utsutsa wolungama ndi wamphamvuyo kuti ngwoipa?


Ngati Mulungu akhotetsa chiweruzo? Ngati Wamphamvuyonse akhotetsa mlandu?


Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu. Ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.


Uzikhala kutali ndi mlandu wonama; ndipo usapha munthu wosachimwa ndi wolungama; pakuti sindidzayesa wolungama munthu woipa.


Ndipo mkulu wao adzakhala mwa iwo, ndi wolamulira wao adzatuluka pakati pao; ndipo ndidzamyandikitsa iye, ndipo adzayandikira kwa Ine, pakuti iye wolimba mtima kuyandikira kwa Ine ndani? Ati Yehova.


Ndipo anagwa nkhope zao pansi, nati, Mulungu, ndinu Mulungu wa mizimu ya anthu onse, walakwa munthu mmodzi, ndipo kodi mukwiya nalo khamu lonse?


tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;


Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.


Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera chipempherere kuti isavumbe mvula; ndipo siinagwe mvula padziko zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa