Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 18:24 - Buku Lopatulika

24 Kapena alipo olungama makumi asanu m'kati mwa mzinda; kodi mudzaononga, simudzasiya malowo chifukwa cha olungama makumi asanu ali momwemo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Kapena alipo olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi; kodi mudzaononga, simudzasiya malowo chifukwa cha olungama makumi asanu ali momwemo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Nanga patakhala kuti pali anthu 50 osachimwa mumzindamo, kodi mudzaonongabe mzinda wonse? Kodi simudzauleka kuti musunge anthu 50 amenewo?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Nanga bwanji patakhala anthu makumi asanu olungama mu mzindamo? Kodi mudzawonongadi onse osausiyako mzindawo chifukwa cha anthu makumi asanu olungama omwe ali mʼmenemo?

Onani mutuwo Koperani




Genesis 18:24
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anayandikira nati, Kodi mudzaononga olungama pamodzi ndi oipa?


Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?


Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwa khumi m'menemo? Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha khumi.


Choipa chanu chikhoza kuipira munthu wonga inu, ndi chilungamo chanu chikhoza kukomera wobadwa ndi munthu.


Akadapanda Yehova wa makamu kutisiyira otsala ang'onong'ono ndithu, ife tikanakhala ngati Sodomu, ife tikadanga Gomora.


Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ake, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakuchita zolungama, wakufuna choonadi; ndipo ndidzamkhululukira.


nanena, Usaope Paulo; ukaimirira pamaso pa Kaisara; ndipo, taona, Mulungu anakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa