Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 18:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo anati, Ndidzabwera kwa iwe ndithu pakufika nyengo yake; taonani Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndipo Sara anamva pakhomo pa hema amene anali pambuyo pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo anati, Ndidzabwera kwa iwe ndithu pakufika nyengo yake; taonani Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndipo Sara anamva pakhomo pa hema amene anali pambuyo pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Chauta adati, “Ndikukulonjeza kuti pakapita miyezi isanu ndi inai ndidzabweranso, ndipo mkazi wako adzakhala ali ndi mwana wamwamuna.” Sara ankangomvetsera ali kuseri kwa chitseko cha hema.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Tsono mmodzi mwa iwo anati, “Mosakayikira ndidzabweranso pa nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa, ndipo Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna.” Koma Sara amene anali kumbuyo kwa Abrahamu pa khoma la tenti ankamva zonsezi.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 18:10
15 Mawu Ofanana  

Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ndidzachulukitsa ndithu mbeu zako, kuti unyinji wao sudzawerengeka.


Ndipo ndidzamdalitsa iye, ndiponso ndidzakupatsa iwe mwana wamwamuna wobadwa mwa iye, inde, ndidzamdalitsa iye, ndipo adzakhala amake amitundu, mafumu a anthu adzatuluka mwa iye.


Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake.


Koma pangano langa ndidzalimbikitsa ndi Isaki, amene Sara adzakubalira iwe nthawi yomwe ino chaka chamawa.


Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Sara mkazi wako? Ndipo anati, Taonani m'hemamo.


Ndipo Yehova anayang'anira Sara monga momwe anati, ndipo Yehova anamchitira iye monga ananena.


Ndipo Sara anatenga pakati, nambalira Abrahamu mu ukalamba wake mwana wamwamuna, nthawi yomweyo Mulungu anamuuza iye.


Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zekariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.


Komatu uyo wa mdzakazi anabadwa monga mwa thupi; koma iye wa mfuluyo, anabadwa monga mwa lonjezano. Izo ndizo zophiphiritsa;


Koma ife, abale, monga Isaki, tili ana a lonjezano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa