Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 16:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo Hagara anambalira Abramu mwana wamwamuna ndipo Abramu anatcha dzina la mwana wake amene anambalira iye Hagara, Ismaele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo Hagara anambalira Abramu mwana wamwamuna ndipo Abramu anatcha dzina la mwana wake amene anambalira iye Hagara, Ismaele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Tsono Hagara adamubalira Abramu mwana wamwamuna, namutcha dzina loti Ismaele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Tsono Hagara anamuberekera Abramu mwana wamwamuna ndipo Abramu anamutcha mwanayo Ismaeli.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 16:15
13 Mawu Ofanana  

Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Taona, uli ndi pakati, ndipo udzabala mwana wamwamuna; nudzamutcha dzina lake Ismaele; chifukwa Yehova anamva kusauka kwako.


Chifukwa chake chitsimecho chinatchedwa Beere-Lahai-Roi; taonani chili pakati pa Kadesi ndi Beredi.


Ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi chimodzi, pamene Hagara anambalira Abramu Ismaele.


Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, Ha! Ismaele akhale ndi moyo pamaso panu!


Koma za Ismaele, ndamvera iwe: taona, ndamdalitsa iye, ndipo ndidzamchulukitsa iye ndithu; adzabala akalonga khumi ndi awiri, ndipo ndidzamuyesa iye mtundu waukulu.


Mibadwo ya Ismaele mwana wamwamuna wa Abrahamu, amene Hagara Mwejipito mdzakazi wa Sara anambalira Abrahamu ndi iyi:


Ndipo ana ake Isaki ndi Ismaele anamuika iye m'phanga la Makipela, m'munda wa Efuroni mwana wake wa Zohari Muhiti, umene uli patsogolo pa Mamure;


ndipo Esau ananka kwa Ismaele, naonjezera kwa akazi amene anali nao, natenga Mahalati mwana wamkazi wa Ismaele mwana wa Abrahamu, mlongo wake wa Nebayoti akhale mkazi wake.


Tiyeni timgulitse iye kwa Aismaele, tisasamulire iye manja; chifukwa ndiye mbale wathu, thupi lathu. Ndipo anamvera iye abale ake.


Ana a Abrahamu: Isaki, ndi Ismaele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa