Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Filemoni 1:22 - Buku Lopatulika

22 Koma undikonzerenso pogona; pakuti ndiyembekeza kuti mwa mapemphero anu ndidzapatsidwa kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Koma undikonzerenso pogona; pakuti ndiyembekeza kuti mwa mapemphero anu ndidzapatsidwa kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Kanthu kenanso ndi aka: undikonzere malo, chifukwa ndikhulupirira kuti Mulungu adzamvera mapemphero a inu nonse, ndi kundibwezera kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Chinthu chinanso ndi ichi: undikonzere malo, chifukwa ndikukhulupirira kuti Mulungu adzamvera mapemphero anu ndi kundibwezera kwa inu.

Onani mutuwo Koperani




Filemoni 1:22
13 Mawu Ofanana  

nanena, Usaope Paulo; ukaimirira pamaso pa Kaisara; ndipo, taona, Mulungu anakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi.


Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m'chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.


pamene paliponse ndidzapita ku Spaniya. Pakuti ndiyembekeza kuonana ndi inu pa ulendo wanga, ndi kuperekezedwa ndi inu panjira panga kumeneko, ngati nditayamba kukhuta pang'ono ndi kukhala ndi inu.


pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri chifukwa cha ife.


Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu;


koma ndikhulupirira mwa Ambuye kuti ine ndekhanso ndidzadza msanga.


Ndipo ndikudandaulirani koposa kuchita ichi, kuti kubwera kwanga kwa inu kufulumidwe.


Zindikirani kuti mbale wathu Timoteo wamasulidwa; pamodzi ndi iye, ngati akudza msanga, ndidzakuonani inu.


Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.


Pokhala ndili nazo zambiri zakukulemberani, sindifuna kuchita ndi kalata ndi kapezi; koma ndiyembekeza kudza kwa inu, ndi kulankhula popenyana, kuti chimwemwe chanu chikwanire.


koma ndiyembekeza kukuona iwe msanga, ndipo tidzalankhula popenyana.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa