Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 9:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo anatenga phulusa la m'ng'anjo, naima pamaso pa Farao; ndi Mose analiwaza kuthambo; ndipo linakhala zilonda zobuka ndi matuza pa anthu ndi pa zoweta.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo anatenga phulusa la m'ng'anjo, naima pamaso pa Farao; ndi Mose analiwaza kuthambo; ndipo linakhala zilonda zobuka ndi matuza pa anthu ndi pa zoweta.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Choncho Mose adatapa phulusalo pa moto ndipo adakaimirira pamaso pa Farao. Adawaza phulusalo kumwamba, ndipo padabuka zithupsa zimene zidaphulika ndi kusanduka zilonda pa anthu ndi pa nyama zomwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Kotero anatenga phulusa la pa moto ndi kuyima pamaso pa Farao. Mose analiwaza mmwamba, ndipo panabuka zotupa zophulika zokha pa munthu aliyense ndi pa ziweto.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 9:10
4 Mawu Ofanana  

Ndipo alembi sanathe kuima pamaso pa Mose chifukwa cha zilondazo; popeza panali zilonda pa alembi ndi pa Aejipito onse.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Tengani phulusa la ng'anjo lodzala manja; ndi Mose aliwaze kuthambo pamaso pa Farao.


Ndipo lidzakhala fumbi losalala padziko lonse la Ejipito, ndipo lidzakhala pa anthu ndi pa zoweta ngati zilonda zobuka ndi matuza, m'dziko lonse la Ejipito.


Yehova adzakukanthani ndi zilombo za ku Ejipito, ndi nthenda yotuluka mudzi, ndi chipere, ndi mphere, osachira nazo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa