Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 40:13 - Buku Lopatulika

13 Nuveke Aroni chovala zopatulikazo; ndi kumdzoza, ndi kumpatula andichitire Ine ntchito ya nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Nuveke Aroni chovala zopatulikazo; ndi kumdzoza, ndi kumpatula andichitire Ine ntchito ya nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Aroniyo umuveke zovala zopatulika. Umdzoze, ndipo umpatule kuti akhale wansembe wonditumikira Ine.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Kenaka umuveke Aaroni zovala zopatulika, umudzoze ndi kumupatula kotero kuti athe kunditumikira monga wansembe.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 40:13
13 Mawu Ofanana  

Ndipo uveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ake omwe; ndi kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lao, ndi kuwapatula, andichitire Ine ntchito ya nsembe.


Pamenepo utenge mafuta odzoza nao nuwatsanulire pamutu pake, ndi kumdzoza.


Ndipo ubwere nao ana ake aamuna ndi kuwaveka malaya am'kati;


Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;


Ili ndi gawo la Aroni, ndi gawo la ana ake, lochokera ku nsembe zamoto za Yehova, analinena, tsiku limene Iye anawasendeza alowe utumiki wa ansembe a Yehova;


limene Yehova analamula ana a Israele aziwapatsa, tsiku limene Iye anawadzoza. Likhale lemba losatha mwa mibadwo yao.


Ndipo Mose anatenga ana a Aroni, nawaveka malaya a m'kati, nawamanga m'chuuno ndi mipango, nawamanga akapa; monga Yehova adzauza Mose.


Ndipo chifukwa cha iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m'choonadi.


Pakuti Iye amene Mulungu anamtuma alankhula mau a Mulungu; pakuti sapatsa Mzimu ndi muyeso.


Ndi chifuniro chimenecho tayeretsedwa mwa chopereka cha thupi la Yesu Khristu, kamodzi, kwatha.


ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene anayeretsedwa nao chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo;


Ndipo inu muli nako kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo mudziwa zonse.


Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa