Eksodo 4:14 - Buku Lopatulika14 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unamyakira Mose, ndipo anati, Nanga Aroni Mlevi mbale wako sialipo kodi? Ndidziwa kuti kulankhula alankhula. Ndipo, taona, atuluka kudzakomana ndiwe; ndipo pakuona iwe adzakondwera m'mtima mwake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unamyakira Mose, ndipo anati, Nanga Aroni Mlevi mbale wako sialipo kodi? Ndidziwa kuti kulankhula alankhula. Ndipo, taona, atuluka kudzakomana ndiwe; ndipo pakuona iwe adzakondwera m'mtima mwake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Pompo Chauta adamkalipira Mose, namufunsa kuti, “Bwanji mbale wako Aroni, Mlevi uja? Ndikudziŵa kuti angathe kulankhula bwino kwambiri. Iyeyo akubwera kudzakumana nawe, ndipo adzakondwa kwambiri pokuwona. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Kenaka Yehova anamupsera mtima Mose ndipo anati, “Kodi suli ndi mʼbale wako Aaroni wa fuko la Levi? Ine ndikudziwa kuti iye amayankhula bwino. Iye wanyamuka kale kudzakumana nawe ndipo adzasangalala akadzakuona. Onani mutuwo |