Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 4:14 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Kenaka Yehova anamupsera mtima Mose ndipo anati, “Kodi suli ndi mʼbale wako Aaroni wa fuko la Levi? Ine ndikudziwa kuti iye amayankhula bwino. Iye wanyamuka kale kudzakumana nawe ndipo adzasangalala akadzakuona.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

14 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unamyakira Mose, ndipo anati, Nanga Aroni Mlevi mbale wako sialipo kodi? Ndidziwa kuti kulankhula alankhula. Ndipo, taona, atuluka kudzakomana ndiwe; ndipo pakuona iwe adzakondwera m'mtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unamyakira Mose, ndipo anati, Nanga Aroni Mlevi mbale wako sialipo kodi? Ndidziwa kuti kulankhula alankhula. Ndipo, taona, atuluka kudzakomana ndiwe; ndipo pakuona iwe adzakondwera m'mtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Pompo Chauta adamkalipira Mose, namufunsa kuti, “Bwanji mbale wako Aroni, Mlevi uja? Ndikudziŵa kuti angathe kulankhula bwino kwambiri. Iyeyo akubwera kudzakumana nawe, ndipo adzakondwa kwambiri pokuwona.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 4:14
19 Mawu Ofanana  

Yehova anapsera mtima Uza chifukwa chochita chinthu chosayenera kuchitika. Choncho Mulungu anamukantha ndipo anafera pomwepo pambali pa Bokosi la Mulungulo.


Choncho Yehova anakwiyira Solomoni chifukwa mtima wake unatembenuka kuchoka kwa Yehova Mulungu wa Israeli, amene anamuonekera kawiri konse.


Lamulo limeneli silinakomerenso Mulungu. Kotero Iye analanga Israeli.


Yehova anatuma Mose mtumiki wake, ndi Aaroni amene Iye anamusankha.


Koma Mose anati, “Chonde Ambuye, pepani, tumani wina kuti akachite zimenezi.”


Koma utenge ndodo imene ili mʼdzanja lakoyo kuti ukachite nayo zizindikiro zozizwitsa.”


Yehova anati kwa Aaroni, “Pita ku chipululu ukakumane ndi Mose.” Iye anapitadi nakakumana ndi Mose pa phiri la Mulungu namupsompsona.


Iwowo anafunsa kuti, “Kodi Yehova anayankhula kudzera mwa Mose yekha? Kodi sanayankhule kudzeranso mwa ife?” Ndipo Yehova anamva zimenezi.


Pakuti zinakomera Mzimu Woyera ndiponso ife kuti tisakusenzetseni katundu wina, kupatula zoyenera zokhazi:


ndinasowa mtendere mu mtima mwanga, chifukwa sindinapezeko mʼbale wanga Tito. Choncho ndinatsanzikana ndi anthu kumeneko nʼkupita ku Makedoniya.


Pakuti aliyense amangofuna zokomera iye yekha osati zokomera Yesu Khristu.


“ ‘Kenaka ndinatuma Mose ndi Aaroni, ndipo ine ndinazunza Aigupto. Pambuyo pake ndinakutulutsani.


“Yakobo atapita ku dziko la Igupto, Aiguptowo akuwazunza, iwo analirira kwa Yehova kuti awathandize, ndipo Yehova anatumiza Mose ndi Aaroni, amene anatulutsa makolo anu mʼdziko la Igupto ndi kudzawakhazika pa malo ano.


Tsiku lina munthu wa Mulungu anabwera kwa Eli ndipo anamuwuza kuti, “Yehova akuti, ‘Kodi Ine sindinadziwulule ndekha kwa banja la kholo lako pamene iwo anali akapolo a Farao ku Igupto?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa