Eksodo 4:11 - Buku Lopatulika11 Koma Yehova ananena naye, Anampangira munthu m'kamwa ndani? Kapena analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Si ndine Yehova kodi? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Koma Yehova ananena naye, Anampangira munthu m'kamwa ndani? Kapena analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Si ndine Yehova kodi? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Apo Chauta adafunsa Mose kuti, “Kodi adapatsa munthu pakamwa ndani? Ndani amasandutsa munthu kuti akhale wosamva kapena wosalankhula, wopenya kapena wosapenya? Kodi si ndine Chauta amene ndimachita zimenezo? Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Yehova anati kwa iye, “Kodi anapatsa munthu pakamwa ndani? Ndani amasandutsa munthu kuti akhale wosayankhula kapena wosamva? Ndani amapanga munthu kukhala wopenya kapena wosaona? Kodi si Ine Yehova? Onani mutuwo |