Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 39:24 - Buku Lopatulika

24 Napangira pa mkawo wa mwinjiro makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Napangira pa mkawo wa mwinjiro makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Pa mpendero wake wapansi, adalumikizapo zithunzi za makangaza zopangidwa ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Pa mpendero wamʼmunsi wa mkanjowo, analumikiza mphonje zokhala ngati makangadza za nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yofewa yosalala ndi yopetedwa bwino yomwe inazungulira mkanjo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 39:24
5 Mawu Ofanana  

Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake.


Ndipo pa mbinyiru wake upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, pambinyiru pake pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolide pozungulira;


ndi pakati pake polowa mutu, ngati polowa pa malaya ochingirizira, ndipo anabinyira pozungulira polowa pake, pangang'ambike.


Ndipo anapanga miliu ya golide woona, napakiza miliu ndi makangaza, pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, popakiza ndi makangaza.


Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa