Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 37:26 - Buku Lopatulika

26 Ndipo analikuta ndi golide woona, pamwamba pake, ndi mbali zake pozungulira, ndi nyanga zake; ndipo analipangira mkombero wagolide pozungulira pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndipo analikuta ndi golide woona, pamwamba pake, ndi mbali zake pozungulira, ndi nyanga zake; ndipo analipangira mkombero wagolide pozungulira pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Adakuta guwa lonse ndi golide wabwino kwambiri pamwamba pake, pa mbali zake ndi pa nyanga zake zomwe. Kuzungulira guwa lonselo, adalemba mkombero wagolide.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Iwo anakuta guwa lonse ndi golide wabwino kwambiri, pamwamba pake, mbali zonse ndi nyanga zake, ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira guwalo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 37:26
3 Mawu Ofanana  

Ndipo ulikute ndi golide woona, ulikute m'kati ndi kubwalo, nulipangire mkombero wagolide pozungulira pake.


Ndipo anapanga guwa la nsembe lofukizapo la mtengo wakasiya; utali wake mkono, ndi kupingasa kwake mkono, laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono iwiri; nyanga zake zinatuluka m'mwemo.


Ndipo analipangira mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake, pangodya zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri, zikhale zopisamo mphiko kulinyamulira nazo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa