Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 37:19 - Buku Lopatulika

19 pa mphanda imodzi panali zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa; ndi pa mphanda ina zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa zinatero mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikaponyali.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 pa mphanda imodzi panali zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; ndi pa mphanda ina zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa zinatero mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikapo nyali.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Iliyonse mwa nthambizo inali ndi maluŵa atatu, opangidwa ngati maluŵa amtowo, okhala ndi nkhunje ndi maluŵa ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa zinali pa mphanda yoyamba. Pa mphanda yachiwiri panalinso zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa. Ndipo mphanda zonse zisanu ndi imodzi zinali chimodzimodzi ndipo zinatuluka mʼchoyikapo nyalecho.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 37:19
3 Mawu Ofanana  

Ku mphanda ina kukhale zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa; ndi ku mphanda inzake zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa; zitere mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikaponyalicho.


ndi m'mbali zake munatuluka mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za choikaponyali zotuluka m'mbali yake imodzi, ndi mphanda zitatu za choikaponyali zotuluka m'mbali yake ina;


Ndipo pa choikaponyali chomwe panali zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yake ndi maluwa ake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa