Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 36:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo anazipanga zokowera makumi asanu zagolide, namanga nsalu pamodzi ndi zokowerazo; ndipo chihema chinakhala chimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo anazipanga zokowera makumi asanu zagolide, namanga nsalu pamodzi ndi zokowerazo; ndipo Kachisi anakhala mmodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Kenaka adapanga ngoŵe zokoŵera zagolide makumi asanu, nalumikiza nsalu zazikulu ziŵirizo ndi ngoŵezo. Pamenepo chihema cha Chauta chidakhala chimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Kenaka anapanga ngowe zagolide 50 zolumikizira nsalu ziwirizo kotero kuti zinapanga chihema chimodzi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 36:13
5 Mawu Ofanana  

Ndipo uzipanga chihema ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri.


Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolide, ndi kumanga nsaluzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti chihema chikhale chimodzi.


Koma tsopano pali ziwalo zambiri, koma thupi limodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa