Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 34:35 - Buku Lopatulika

35 Ndipo ana a Israele anaona nkhope ya Mose, kuti khungu la nkhope ya Mose linanyezimira; ndipo Mose anaikanso chophimba pankhope pake, kufikira akalowa kulankhula ndi Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Ndipo ana a Israele anaona nkhope ya Mose, kuti khungu la nkhope ya Mose linanyezimira; ndipo Mose anaikanso chophimba pankhope pake, kufikira akalowa kulankhula ndi Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Ndipo anthuwo ankaona kuti nkhope yake njoŵala, koma Moseyo ankadziphimbanso kumaso mpaka nthaŵi ina yakuti apitenso kukalankhula ndi Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 iwo amaona nkhope yake ikunyezimira. Choncho Mose amaphimba nkhope yake ngakhale pamene amapita kukayankhula ndi Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 34:35
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Mose anasonkhanitsa khamu lonse la ana a Israele, nanena nao, Siwa mau amene Yehova analamula, kuti muwachite.


Ndani akunga wanzeru? Ndani adziwa tanthauzo la mau? Nzeru ya munthu iwalitsa nkhope yake, kuduwa kwa nkhope yake ndi kusanduka.


Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi.


Pomwepo olungamawo adzawalitsa monga dzuwa, mu Ufumu wa Atate wao. Amene ali ndi makutu amve.


Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.


Iyeyo anali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu munafuna kukondwera m'kuunika kwake kanthawi.


ndipo si monga Mose, amene anaika chophimba pa nkhope yake, kuti ana a Israele asayang'anitse pa chimaliziro cha chimene chinalikuchotsedwa;


kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa