Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 34:34 - Buku Lopatulika

34 Koma pakulowa Mose pamaso pa Yehova kunena ndi Iye, anachotsa chophimbacho, kufikira akatuluka; ndipo atatuluka analankhula ndi ana a Israele chimene adamuuza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Koma pakulowa Mose pamaso pa Yehova kunena ndi Iye, anachotsa chophimbacho, kufikira akatuluka; ndipo atatuluka analankhula ndi ana a Israele chimene adamuuza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Nthaŵi zonse Moseyo ankati akaloŵa m'chihema kukalankhula ndi Chauta, ankachotsa nsalu yophimba kumaso ija mpaka atatuluka. Tsono atatuluka, ankauza Aisraele aja zonse zimene Chauta wamulamula kuti anene.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Koma nthawi zonse popita pamaso pa Yehova kukayankhula naye amachotsa chophimbacho mpaka atatuluka. Ndipo akatuluka kudzawuza Aisraeli zimene walamulidwa,

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 34:34
4 Mawu Ofanana  

Ndipo ana a Israele anaona nkhope ya Mose, kuti khungu la nkhope ya Mose linanyezimira; ndipo Mose anaikanso chophimba pankhope pake, kufikira akalowa kulankhula ndi Iye.


Koma pamene akatembenukira kwa Ambuye, chophimbacho chichotsedwa.


Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa