Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 34:13 - Buku Lopatulika

13 koma mupasule maguwa a nsembe ao, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 koma mupasule maguwa a nsembe ao, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Muzigwetsa maguwa ao, muwononge miyala yao yopatulika imene adaimiritsa, ndipo mugwetse mitengo yao yopatulika yopembedzerapo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Mukagumule maguwa awo ansembe, mukaswe miyala yawo yachipembedzo, ndipo mukadule mitengo yawo ya Asera.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 34:13
25 Mawu Ofanana  

Popeza Yehova adzawakantha Aisraele monga bango ligwedezeka ndi madzi, nadzazula Aisraele m'dziko lino labwino analipatsa makolo ao, nadzawamwazira ku tsidya lija la Yufurate, popeza iwo anapanga zifanizo zao zokwiyitsa Yehova.


Nagamula fano la Baala, nagamula nyumba ya Baala, naiyesa dzala mpaka lero lino.


Anachotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha chifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israele anaifukizira zonunkhira, naitcha Chimkuwa.


Nathyolathyola zoimiritsa, nalikha zifanizo, nadzaza pamalo pao ndi mafupa a anthu.


nachotsa maguwa a nsembe achilendo, ndi misanje; naphwanya zoimiritsa zao, nalikha zifanizo zao,


Maaka yemwe, mai wake wa Asa, mfumu, namchotsa uyu asakhalenso mai wa ufumu, popeza anapanga fanizo lolaula; ndipo Asa analikha fanizolo, naliphwanyaphwanya, nalitenthera ku mtsinje wa Kidroni.


Ndi mtima wake unakwezeka m'njira za Yehova; anachotsanso misanje ndi zifanizo mu Yuda.


Ndipo anasiya nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo ao, natumikira zifanizo, ndi mafano; ndipo mkwiyo unawagwera Yuda ndi Yerusalemu, chifukwa cha kupalamula kwao kumene.


Chitatha ichi chonse tsono, Aisraele onse opezekako anatuluka kunka kumizinda ya Yuda, naphwanya zoimiritsa, nalikha zifanizo, nagamula misanje ndi maguwa a nsembe mu Yuda monse, ndi mu Benjamini, mu Efuremunso, ndi mu Manase, mpaka adaziononga zonse. Pamenepo ana onse a Israele anabwerera, yense kudziko lake ndi kumizinda yao.


Pemphero lake lomwe, ndi m'mene Mulungu anapembedzeka naye, ndi tchimo lake lonse, ndi kulakwa kwake, ndi apo anamanga misanje, naimika zifanizo ndi mafano osema asanadzichepetse, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Hozai.


Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao.


Ndipo iye sadzayang'ana pa maguwa a nsembe, ntchito ya manja ake, ngakhale kulemekeza chimene anachipanga ndi zala zake, ngakhale zifanizo pena mafano a dzuwa.


Chifukwa chake, mwa ichi choipa cha Yakobo chidzafafanizidwa, ndipo ichi ndi chipatso chonse chakuchotsa tchimo lake; pamene iye adzayesa miyala yonse ya guwa la nsembe, ngati miyala yanjeresa yoswekasweka, zifanizo ndi mafano a dzuwa sizidzaukanso konse.


Pokumbukira ana ao maguwa a nsembe ao ndi zoimiritsa zao kumitengo yaiwisi ya pa zitunda zazitali.


Ndipo ndidzazula zifanizo zako m'kati mwako, ndi kutha mizinda yako.


mupirikitse onse okhala m'dziko pamaso panu, ndi kuononga mafano ao onse a miyala, ndi kuononga mafano ao onse oyenga, ndi kupasula misanje yao yonse;


Musazike kwa inu nokha mzati wa Ashera, wa mtengo uliwonse, pafupi pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, limene mwadzimangira.


Ndipo musamadziutsira choimiritsa chilichonse chimene Yehova Mulungu wanu adana nacho.


Koma muzichita nao motero: mukapasule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao, ndi kutentha mafano ao osema ndi moto.


ndipo inu, musamachita pangano ndi nzika za m'dziko ili; muzigamula maguwa ao a nsembe. Koma simunamvere mau anga; mwachichita ichi chifukwa ninji?


Ndipo kunali, usiku womwe uja Yehova ananena naye, Tenga ng'ombe ya atate wako, ndiyo ng'ombe yachiwiri ya zaka zisanu ndi ziwiri, nugamule guwa la nsembe la Baala ndilo la atate wako, nulikhe chifanizo chili pomwepo;


numangire Yehova Mulungu wako guwa la nsembe pamwamba pa lingali, monga kuyenera; nutenge ng'ombe yachiwiriyo, nufukize nsembe yopsereza; nkhuni zake uyese chifanizo walikhacho.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa