Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 32:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo Mose anatembenuka, natsika m'phirimo, magome awiri a mboni ali m'dzanja lake; magome olembedwa kwina ndi kwina; analembedwa mbali ina ndi inzake yomwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo Mose anatembenuka, natsika m'phirimo, magome awiri a mboni ali m'dzanja lake; magome olembedwa kwina ndi kwina; analembedwa mbali ina ndi inzake yomwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Mose adabwerera natsika phiri atanyamula miyala iŵiri ija yaumboni, yolembedwa mbali zonse ziŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Mose anatembenuka ndi kutsika phiri miyala iwiri ya pangano ili mʼmanja mwake. Miyalayi inalembedwa mbali zonse, kutsogolo ndi kumbuyo komwe.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 32:15
14 Mawu Ofanana  

Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru.


Monga Yehova analamula Mose, momwemo Aroni anauika patsogolo pa Mboni, usungikeko.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa Ine m'phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi chilamulo ndi malamulo ndawalembera kuti uwalangize.


Ndipo Mose analowa m'kati mwa mtambo, nakwera m'phirimo; ndipo Mose anakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku.


Ndipo atatha Iye kulankhula ndi Mose, paphiri la Sinai, anampatsa magome awiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu.


Ndipo magomewo ndiwo ntchito ya Mulungu, kulembaku ndiko kulemba kwa Mulungu, kozokoteka pa magomewo.


Ndipo kunali pakutsika Mose paphiri la Sinai, ndi magome awiri a mboni m'dzanja lake la Mose, pakutsika iye m'phirimo, Mose sanadziwe kuti khungu la nkhope yake linanyezimira popeza Iye adalankhula naye.


Ndipo anatenga mboniyo, naiika m'likasa, napisa mphiko palikasa, naika chotetezerapo pamwamba pa likasa;


popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata ya Khristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m'magome amiyala, koma m'magome a mitima yathupi.


Koma ngati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolochedwa m'miyala, unakhala mu ulemerero, kotero kuti ana a Israele sanathe kuyang'anitsa pa nkhope yake ya Mose, chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake, umene unalikuchotsedwa:


Yehova ananena mau awa kwa msonkhano wanu wonse, m'phirimo ali pakati pa moto, pamtambo, pamdima bii, ndi mau aakulu; osaonjezapo kanthu. Ndipo anawalembera pa magome awiri amiyala, nandipatsa awa.


Pamenepo ndinatembenuka ndi kutsika m'phiri, ndi phirilo linatentha ndi moto; ndi magome awiri a chipangano anali m'manja mwanga.


okhala nayo mbale ya zofukiza yagolide ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golide, momwemo munali mbiya yagolide yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaaphukayo, ndi magome a chipangano;


Ndipo ndinaona m'dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu buku lolembedwa m'kati ndi kunja kwake, losindikizika ndi zizindikiro zisanu ndi ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa