Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 29:22 - Buku Lopatulika

22 Utengenso mafuta a nkhosa yamphongoyo, ndi mchira, chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pamenepo, ndi mwendo wam'mwamba wa ku dzanja lamanja; pakuti ndiyo nkhosa yamphongo ya kudzaza manja;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Utengenso mafuta a nkhosa yamphongoyo, ndi mchira, chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pamenepo, ndi mwendo wam'mwamba wa ku dzanja lamanja; pakuti ndiyo nkhosa yamphongo ya kudzaza manja;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 “Nkhosa yamphongo ija utengeko mafuta ake, mchira wake wamafuta, mafuta okuta matumbo, mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, imso ziŵiri ndi mafuta ozikutawo, ndiponso ntchafu ya ku dzanja lamanja, chifukwa nkhosa imeneyi ndi nsembe ya pa mwambo wodzozera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 “Pa nkhosa yayimuna ija utengepo mafuta ake, mafuta a ku mchira wake, mafuta okuta matumbo, mafuta okuta chiwindi, impsyo zonse ziwiri ndi mafuta ake, ndiponso ntchafu yakumanja. Iyi ndi nkhosa ya mwambo wodzoza.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 29:22
14 Mawu Ofanana  

Nutenge mafuta onse akukuta matumbo, ndi chokuta cha mphafa ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pa izo, ndi kuzitentha paguwa la nsembe.


Ndipo utapeko pamwazi uli paguwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nao, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zovala zake zomwe, ndi ana ake aamuna ndi zovala zao zomwe pamodzi ndi iye.


ndi mkate wamphumphu umodzi, ndi kamtanda ka mkate wosakaniza ndi mafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, zili mu dengu la mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova;


Ndi nganga yoweyula ndi mwendo wokweza mudyere izi pamalo poyera; iwe ndi ana ako aamuna, ndi ana ako aakazi omwe, popeza zapatsidwa gawo lako ndi gawo la ana ako aamuna, zochokera ku nsembe zoyamika za ana a Israele.


ndipo wansembe atenge mwanawankhosa mmodzi wamwamuna, nabwere naye akhale nsembe yopalamula, pamodzi ndi muyeso uja wa mafuta, naziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.


Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova; yotengako ku nsembe yoyamika; mafuta ake, mchira wamafuta wonse, atauchotsa kufupi ku fupa la msana; naichotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,


Ndipo achotseko, nabwere nao mafuta ake onse; mchira wamafuta, ndi mafuta akukuta matumbo,


Icho ndi chilamulo cha nsembe yopsereza, cha nsembe yaufa, cha nsembe yauchimo, ndi cha nsembe yopalamula, ndi cha kudzaza dzanja, ndi cha nsembe zoyamika;


ndi mafuta a ng'ombe; ndi a nkhosa yamphongoyo, ndi mchira wamafuta, ndi chophimba matumbo, ndi impso, ndi chokuta cha mphafa;


Ndipo Aroni anaweyula ngangazo ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; monga Iye anauza Mose.


Ndipo nyama yake ndi yako, ndiyo nganga ya nsembe yoweyula ndi mwendo wathako wa kulamanja, ndizo zako.


Ndipo wophikayo ananyamula mwendo ndi mnofu wake, nauika pamaso pa Saulo. Ndipo Samuele anati, Onani chimene tinakuikirani? Muchiike pamaso panu, nudye; pakuti ichi anakuikirani kufikira nthawi yonenedwa, popeza ndinati, Ndinaitana anthuwo. Chomwecho Saulo anadya ndi Samuele tsiku lija.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa