Eksodo 29:21 - Buku Lopatulika21 Ndipo utapeko pamwazi uli paguwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nao, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zovala zake zomwe, ndi ana ake aamuna ndi zovala zao zomwe pamodzi ndi iye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201421 Ndipo utapeko pamwazi uli pa guwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nao, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zovala zake, ndi pa ana ake amuna, ndi pa zovala za ana ake amuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zovala zake zomwe, ndi ana ake amuna ndi zovala zao zomwe pamodzi ndi iye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa21 Utengeko magazi otsalira pa guwa ndiponso mafuta ena odzozera, uwaze Aroni ndi zovala zake. Uwazenso ana ake ndi zovala zao. Tsono iyeyo ndi ana ake adzakhala opatulika, pamodzi ndi zovala zomwezo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero21 Ndipo utenge magazi ena amene ali pa guwa lansembe komanso pa mafuta ena odzozera ndipo uwawaze pa Aaroni ndi zovala zake ndi ana ake ndi zovala zawo. Ndiye kuti iyeyo ndi ana ake aamuna adzakhala opatulika pamodzi ndi zovala zawo. Onani mutuwo |
Pamenepo uiphe nkhosa yamphongoyo, nutapeko pa mwazi wake, ndi kuupaka pa ndewerere ya khutu lamanja la Aroni, ndi pa ndewerere ya khutu lamanja ana ake aamuna, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lao lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao lamanja ndi kuuwaza mwaziwo paguwa la nsembe posungulira.