Eksodo 29:20 - Buku Lopatulika20 Pamenepo uiphe nkhosa yamphongoyo, nutapeko pa mwazi wake, ndi kuupaka pa ndewerere ya khutu lamanja la Aroni, ndi pa ndewerere ya khutu lamanja ana ake aamuna, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lao lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao lamanja ndi kuuwaza mwaziwo paguwa la nsembe posungulira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Pamenepo uiphe nkhosa yamphongoyo, nutapeko pa mwazi wake, ndi kuupaka pa ndewerere ya khutu lamanja la Aroni, ndi pa ndewerere ya khutu lamanja ana ake amuna, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lao lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao lamanja ndi kuuwaza mwaziwo pa guwa la nsembe posungulira. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Muiphe, ndipo mutengeko magazi ake ndi kupaka pa khutu la ku dzanja lamanja la Aroni, ndi pa khutu la ku dzanja lamanja la ana ake aamuna. Upakenso pa chala chao chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja. Magazi ena uwaze pa mbali zonse za guwa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 Uyiphe ndipo utenge magazi ake ena ndi kupaka ndewere za makutu a kudzanja lamanja la Aaroni ndi ana ake aamuna. Upakenso pa zala zawo zazikulu za kudzanja lawo lamanja, ndi zala zazikulu za kuphazi lakudzanja lawo lamanja. Kenaka uwaze magazi otsalawo mbali zonse za guwalo. Onani mutuwo |