Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 27:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yotsekera ya mikono makumi awiri, ya lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula; nsichi zake zikhale zinai, ndi makamwa ao anai.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yotsekera ya mikono makumi awiri, ya lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula; nsichi zake zikhale zinai, ndi makamwa ao anai.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yochinga yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndi ya bafuta wosalala, wopikidwa bwino ndi wopetedwa mwaluso. Kutalika kwake kukhale mamita asanu ndi anai. Ikhale ndi nsanamira zinai zomangidwa pa masinde anai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 “Pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yotchinga yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira ndiponso yofewa yosalala. Nsaluyo ikhale yotalika mamita asanu ndi anayi, yopangidwa ndi anthu aluso. Pakhalenso mizati yake inayi ndi matsinde akenso anayi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 27:16
10 Mawu Ofanana  

Adzamtsogolera kwa mfumu wovala zamawangamawanga, anamwali anzake omtsata adzafika nao kwa inu.


Ndipo uziomba nsalu yotchinga ya thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi la bafuta wa thonje losansitsa, aiombe ndi akerubi ntchito ya mmisiri;


Ndipo uziomba nsalu yotsekera pa khomo la hema, ya lakuda, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula.


Ndi pa mbali ina pakhale nsalu zotchingira za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zikhale zitatu, ndi makamwa ao atatu.


Nsichi zonse za pabwalo pozungulira zimangike pamodzi ndi mitanda yasiliva; zokowera zao zasiliva, ndi makamwa ao amkuwa.


Ndipo upikule malaya am'kati abafuta a thonje losansitsa, nusoke nduwira wabafuta, nusokenso mpango wopikapika.


Ndipo anaomba nsalu yotsekera pa khomo la chihemacho, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula;


ndi mpango wabafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ntchito ya wopikula; monga Yehova adamuuza Mose.


ndi nsalu zotchinga za kubwalo, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, lokhala ku chihema, ndi ku guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zake za ku ntchito zake zonse.


Kodi sanapeze, sanagawe zofunkha? Namwali, anamwali awiri kwa munthu aliyense. Chofunkha cha nsalu za mawangamawanga kwa Sisera; chofunkha cha nsalu za mawangamawanga, za maluwa, nsalu za mawangamawanga, za maluwa konsekonse, kwa chofunkha cha khosi lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa