Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 27:17 - Buku Lopatulika

17 Nsichi zonse za pabwalo pozungulira zimangike pamodzi ndi mitanda yasiliva; zokowera zao zasiliva, ndi makamwa ao amkuwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Nsichi zonse za pabwalo pozungulira zimangike pamodzi ndi mitanda yasiliva; zokowera zao zasiliva, ndi makamwa ao amkuwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Nsanamira zonse kuzungulira bwalolo zilumikizidwe ndi mitanda yasiliva, ndipo ngoŵe zake zikhalenso zasiliva, koma masinde ake akhale amkuŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Mizati yonse yozungulira bwalolo ilumikizidwe ndi zingwe zasiliva. Ngowe zake zikhale zasiliva, koma matsinde ake akhale amkuwa.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 27:17
4 Mawu Ofanana  

Ndipo pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yotsekera ya mikono makumi awiri, ya lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula; nsichi zake zikhale zinai, ndi makamwa ao anai.


Utali wake wa bwalolo ukhale wa mikono zana limodzi, ndi kupingasa kwake makumi asanu monsemo, ndi msinkhu wake wa mpanda mikono isanu; ukhale wabafuta wa thonje losansitsa; ndi makamwa a nsichizo akhale amkuwa.


Ndipo anapanga zokowera za mizati nsanamira ndi nsichi ndi masekeli aja chikwi chimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu asanu, nakuta mitu yake, nazigwirizanitsa pamodzi.


Ndipo anapanga nao makamwa a pa khomo la chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe lamkuwa, ndi sefa wake amkuwa, ndi zipangizo zonse za guwa la nsembe,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa