Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 21:8 - Buku Lopatulika

8 Akapanda kumkonda mbuye wake, amene anamtoma mwini yekha, azilola kuti amuombole; alibe mphamvu yakumgulitsa kwa anthu achilendo, popeza wachita naye monyenga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Akapanda kumkonda mbuye wake, amene anamtoma mwini yekha, azilola kuti amuombole; alibe mphamvu yakumgulitsa kwa anthu achilendo, popeza wachita naye monyenga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Ngati mkaziyo amuipira m'maso mbuye amene ankafuna kumkwatirayo, amlole kuti aomboledwe. Sangathe konse kumgulitsa kwa anthu achilendo chifukwa chakuti sadamchite zokhulupirika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Koma ngati mkaziyo sakukondweretsa bwana wake amene wamusankha kuti amukwatire, amulole kuti awomboledwe. Bwanayo alibe mphamvu zomugulitsa kwa anthu achilendo, chifukwa iyeyo waphwanya pangano lake lomukwatira iye.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 21:8
13 Mawu Ofanana  

ndipo Esau anaona kuti ana aakazi a Kanani sanakondweretse Isaki atate wake:


Abale anga anachita monyenga ngati kamtsinje, ngati madzi a timitsinje akupitirira.


Ndipo munthu akagulitsa mwana wake wamkazi akhale mdzakazi, iyeyu asatuluke monga amatuluka anyamata.


Koma ngati amtomera mwana wake wamwamuna, amchitire monga kuyenera ana aakazi.


Ndipo Mose anati, Onani, ndilikutuluka ine kwanu, ndidzapemba Yehova kuti mizaza ichoke mawa kwa Farao, ndi kwa anyamata ake, ndi kwa anthu ake; komatu, Farao asanyengenso ndi kukana kulola anthuwa amuke kukamphera nsembe Yehova.


Ndipo ndidzasandutsa dziko chipululu; popeza anachita cholakwa, ati Ambuye Yehova.


Ndipo munthuyo ndani anapala bwenzi ndi mkazi osamtenga? Amuke nabwerere kunyumba kwake, kuti angafe kunkhondo, nangamtenge munthu wina.


Koma atate wake ndi amai wake ananena naye, Kodi palibe mkazi mwa ana aakazi a abale ako, kapena mwa anthu a mtundu wanga onse, kuti wamuka kutenga mkazi wa Afilisti osadulidwawo? Nati Samisoni kwa atate wake, Nditengereni iye, pakuti andikonda pamaso panga.


ngati tsono mwachitira Yerubaala ndi nyumba yake zoona ndi zangwiro lero lino, kondwerani naye Abimeleki, nayenso akondwere nanu;


Koma Saulo anakwiya ndithu, ndi kunenaku kunamuipira; nati, Kwa Davide anawerengera zikwi zankhani, koma kwa ine zikwi zokha; chimperewera nchiyaninso, koma ufumu wokha?


Koma chimenechi sichinakondweretse Samuele, pamene iwo anati, Tipatseni mfumu kuti itiweruze. Ndipo Samuele anapemphera kwa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa