Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 14:24 - Buku Lopatulika

24 Ndipo kunali, ulonda wa mamawa, Yehova ali m'moto ndi m'mtambo njo anapenyera pa ulendo wa Aejipito, nauvuta ulendo wa Aejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndipo kunali, ulonda wa mamawa, Yehova ali m'moto ndi m'mtambo njo anapenyera pa ulendo wa Aejipito, nauvuta ulendo wa Aejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Tsono kusanache m'maŵa ndithu, Chauta, ali m'chipilala chamtambo ndi chamoto, adayang'ana ankhondo a Aejipito ndipo adaŵachititsa mantha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Kutatsala pangʼono kucha, Yehova ali mu chipilala chamoto ndi chamtambo, anayangʼana asilikali ankhondo a Igupto ndipo anabweretsa chisokonezo pakati pawo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 14:24
16 Mawu Ofanana  

Ndipo ukuti, Adziwa chiyani Mulungu? Aweruza kodi mwa mdima wa bii?


M'kamphindi akufa, ngakhale pakati pa usiku, anthu agwedezeka, napita, amphamvu achotsedwa opanda dzanja lakuwachotsa.


Iye akapatsa mpumulo adzamtsutsa ndani? Akabisa nkhope yake adzampenyerera ndani? Chikachitika pa mtundu wa anthu, kapena pa munthu, nchimodzimodzi;


Upenyerere aliyense wodzikuza, numtsitse, nupondereze oipa pomwe akhala.


amene apenyerera padziko lapansi, ndipo linjenjemera; akhudza mapiri, ndipo afuka.


Anapenya mudziwo, ndipo pamenepo anadabwa; anaopsedwa, nathawako.


Ndipo msana anawatsogolera ndi mtambo ndi usiku wonse ndi kuunika kwa moto.


Pakuti pamaso panu zaka zikwi zikhala ngati dzulo, litapita, ndi monga ulonda wa usiku.


Ndipo Yehova anawatsogolera usana ndi mtambo njo kuwatsogolera m'njira; ndi usiku ndi moto njo, wakuwawalitsira; kuti ayende usana ndi usiku;


Ndipo anagulula njinga za magaleta ao, nawayendetsa molemetsa; pamenepo Aejipito anati, Tithawe pamaso pa Israele; pakuti Yehova alikuwagwirira nkhondo pa Aejipito.


Angakhale alowa ndende pamaso pa adani ao, kumeneko ndidzalamulira lupanga, ndipo lidzawapha; ndipo ndidzayang'anitsa maso anga kwa iwowa, kuwachitira choipa, si chokoma ai.


Ndipo m'mawa mwake Saulo anagawa anthu magulu atatu; ndipo iwowa anafika pakati pa zithandozo mu ulonda wa mamawa, nakantha Aamoni kufikira kutentha kwa dzuwa. Ndipo otsalawo anabalalika, osatsala pamodzi ngakhale awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa