Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 12:42 - Buku Lopatulika

42 Ndiwo usiku wosungira Yehova ndithu, chifukwa cha kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; usiku womwe uno ukhale wosungira Yehova ana onse a Israele ku mibadwo yao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

42 Ndiwo usiku wosungira Yehova ndithu, chifukwa cha kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; usiku womwe uno ukhale wosungira Yehova ana onse a Israele ku mibadwo yao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

42 Usiku wonse Chauta adachezera kutulutsa Aisraelewo m'dziko lija la Ejipito. Nchifukwa chake usiku umenewu ndi wopatulikira Chauta pa mibadwo yonse, kuti ukhale usiku womwe Aisraele onse ayenera kuchezera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

42 Usiku wonse Yehova anachezera kutulutsa ana a Israeli mʼdziko la Igupto. Nʼchifukwa chake pa tsiku limeneli Aisraeli onse azichezera usiku wonse kulemekeza Mulungu kamba ka mibado yonse ya mʼtsogolo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 12:42
6 Mawu Ofanana  

Natulutsa Israele pakati pao; pakuti chifundo chake nchosatha.


Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.


Chifukwa chake uzikasunga lemba ili pa nyengo yake chaka ndi chaka.


Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa.


Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa. Uzidya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri, monga ndakuuza pa nthawi yonenedwa, m'mwezi wa Abibu; pakuti mwezi wa Abibu unatuluka mu Ejipito.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa