Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Chivumbulutso 2:2 - Buku Lopatulika

2 Ndidziwa ntchito zako, ndi chilemetso chako ndi chipiriro chako ndi kuti sungathe kulola oipa, ndipo unayesa iwo amene adzitcha okha atumwi, osakhala atumwi, nuwapeza onama;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndidziwa ntchito zako, ndi chilemetso chako ndi chipiriro chako ndi kuti sukhoza kulola oipa, ndipo unayesa iwo amene adzitcha okha atumwi, osakhala atumwi, nuwapeza onama;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndikudziŵa kuti mwakhala mukugwira ntchito kolimba, ndipo kuti muli ndi kupirira kosatepatepa. Ndikudziŵanso kuti anthu ochimwa simungaŵalekerere. Anthu amene amadzitcha atumwi, pamene sali atumwi konse, mwaŵayesa, ndipo mwaŵapeza kuti ngonama.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ine ndimadziwa zochita zako, ntchito yako yowawa ndi kupirira kwako. Ine ndimadziwa kuti sungalekerere anthu oyipa amene amadzitcha atumwi pamene sichoncho, unawayesa, ndipo unawapeza kuti ndi abodza.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 2:2
21 Mawu Ofanana  

Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama; koma mayendedwe a oipa adzatayika.


Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziweni inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika.


Koma ananena ichi kuti amuyese; pakuti anadziwa yekha chimene adzachita.


umene suli wina; koma pali ena akuvuta inu, nafuna kuipsa Uthenga Wabwino wa Khristu.


Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;


ndi kukumbukira kosalekeza ntchito yanu ya chikhulupiriro, ndi chikondi chochitachita, ndi chipiriro cha chiyembekezo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu Atate wathu;


Yesani zonse; sungani chokomacho,


Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.


pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.


Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.


Potero kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba; koma ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa choikaponyali chako, kuchichotsa pamalo pake, ngati sulapa.


Koma ichi uli nacho, kuti udana nazo ntchito za Anikolai, zimene Inenso ndidana nazo.


Ndidziwa chisautso chako, ndi umphawi wako (komatu uli wachuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana.


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Sardi lemba: Izi anena Iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri: Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa.


Ndidziwa ntchito zako, kuti suli wozizira kapena wotentha: mwenzi utakhala wozizira kapena wotentha.


Ndidziwa ntchito zako (taona, ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sangathe kutsekapo), kuti uli nayo mphamvu pang'ono, ndipo unasunga mau anga, osakana dzina langa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa