Chivumbulutso 11:3 - Buku Lopatulika3 Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri amphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri amphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Ndidzatuma mboni zanga ziŵiri zovala chiguduli, kuwonetsa chisoni, kuti zidzalalike mau ochokera kwa Mulungu pa masiku 1,260.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Ndipo ndidzapereka mphamvu kwa mboni zanga ziwiri, zitavala ziguduli, ndipo kwa masiku 1,260 zidzakhala zikulalikira.” Onani mutuwo |
Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambire chilombo, kapena fano lake, nisanalandire lembalo pamphumi ndi padzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.