Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 11:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo bwalo la kunja kwa Kachisi ulisiye padera, osaliyesa; pakuti adapatsa ilo kwa amitundu; ndipo mzinda wopatulika adzaupondereza miyezi makumi anai mphambu iwiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo bwalo la kunja kwa Kachisi ulisiye padera, osaliyesa; pakuti adapatsa ilo kwa amitundu; ndipo mzinda wopatulika adzaupondereza miyezi makumi anai mphambu iwiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Koma bwalo la kunja kwa Nyumbayo ulisiye, osaliyesa. Bwalo limeneli lidapatsidwa kwa anthu akunja, ndipo iwowo adzaupondereza Mzinda woyerawo pa miyezi 42.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Koma bwalo lakunja ulisiye, usaliyeze chifukwa linaperekedwa kwa a mitundu ina. Iwo adzawupondereza mzinda woyerawo kwa miyezi 42.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 11:2
32 Mawu Ofanana  

Mulungu, akunja alowa m'cholowa chanu; anaipsa Kachisi wanu woyera; anachititsa Yerusalemu bwinja.


Pakuti adziyesa okha a mzinda wopatulika, ndi kudzikhazikitsa iwo okha pa Mulungu wa Israele; dzina lake ndi Yehova wa makamu.


Ndipo tsopano ndidzakuuzani chimene nditi ndichite ndi munda wanga wampesa; ndidzachotsapo tchinga lake, ndipo zidzadyedwa; ndidzagumula linga lake ndipo zidzapondedwa pansi;


Galamuka! Galamuka! Tavala mphamvu zako, Ziyoni; tavala zovala zako zokongola, Yerusalemu, mzinda wopatulika; pakuti kuyambira tsopano sadzalowanso kwa iwe wosadulidwa ndi wodetsedwa.


Amaliwongo atambasulira manja ao pa zokondweretsa zake zonse; pakuti waona amitundu atalowa m'malo ake opatulika, amene munalamulira kuti asalowe mumsonkhano mwanu.


Ndipo utatsiriza awa, ugonerenso mbali yako ya kumanja, ndi kusenza mphulupulu ya nyumba ya Yuda; ndakuikira masiku makumi anai, kuliyesa tsiku limodzi ngati chaka chimodzi.


Analiyesa mbali zake zinai, linali nalo linga pozungulira pake, utali wake mikono mazana asanu, chitando chake mikono mazana asanu, kusiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba.


Ndipo ndinamva munthuyo wovala bafuta wokhala pamwamba pamadzi a mumtsinje, nakweza dzanja lake lamanja ndi lamanzere kumwamba, nalumbira pali Iye wokhala ndi moyo kosatha, kuti zidzachitika nthawi, ndi nthawi zina, ndi nusu; ndipo atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo zidzatha izi zonse.


Pamenepo ndinafuna kudziwa choonadi cha chilombo chachinai chija chidasiyana nazo zonsezi, choopsa chopambana, mano ake achitsulo, ndi makadabo ake amkuwa, chimene chidalusa, ndi kuphwanya, ndi kupondereza zotsala ndi mapazi ake;


Nidzanena mau akutsutsana ndi Wam'mwambamwamba, nidzalemetsa opatulika a Wam'mwambamwamba, nidzayesa kusintha nthawizo ndi chilamulo; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lake mpaka nthawi imodzi, ndi nthawi zina, ndi nthawi yanusu.


Nikula, kufikira khamu la kuthambo; ndi zina za khamulo ndi za nyenyezi inazigwetsa pansi, ndi kuzipondereza.


Pamenepo ndinamva wina woyera alikunena; ndi wina woyera anati kwa iye uja wanenayo, Masomphenya a nsembe yopsereza yachikhalire, ndi cholakwa chakupululutsa cha kupereka malo opatulika ndi khamulo ziponderezedwe, adzakhala mpaka liti?


Nati kwa ine, Mpaka masiku zikwi ziwiri mphambu mazana atatu usana ndi usiku; pamenepo malo opatulika adzayesedwa olungama.


Monga mwa kuwerenga kwa masiku amene munazonda dziko, masiku makumi anai, tsiku limodzi kuwerenga chaka chimodzi, mudzasenza mphulupulu zanu, zaka makumi anai, ndipo mudzadziwa kuti ndaleka lonjezano langa.


ndipo anatuluka m'manda mwao pambuyo pa kuuka kwake, nalowa m'mzinda woyera, naonekera kwa anthu ambiri.


Pamenepo mdierekezi anamuka naye kumzinda woyera; namuika Iye pamwamba penipeni pa Kachisi,


Inu ndinu mchere wa dziko lapansi; koma mcherewo ngati ukasukuluka, adzaukoleretsa ndi chiyani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu.


Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka kumitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza Yerusalemu kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.


ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene anayeretsedwa nao chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo;


Ndipo atapita masiku atatu ndi nusu lake mzimu wamoyo wochokera kwa Mulungu unawalowera, ndipo anakhala chilili; ndipo mantha akulu anawagwera iwo akuwapenya.


Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri amphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli.


Ndipo mkazi anathawira kuchipululu, kumene ali nayo mbuto yokonzekeratu ndi Mulungu, kuti kumeneko akamdyetse masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.


Ndipo ananditenga mu Mzimu kunka kuphiri lalikulu ndi lalitali, nandionetsa mzinda wopatulikawo, Yerusalemu, wotsika mu Mwamba kuchokera kwa Mulungu,


Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake.


ndipo aliyense akachotsako pa mau a buku la chinenero ichi, Mulungu adzamchotsera gawo lake pa mtengo wa moyo, ndi m'mzinda woyerawo, ndi pa izi zilembedwa m'bukumu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa