Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 9:9 - Buku Lopatulika

9 Pakuti taonani, ndidzalamulira, ndipo ndidzapeta nyumba ya Israele mwa amitundu onse, monga apeta tirigu m'lichero; koma silidzagwa pansi diso, ndi limodzi lonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pakuti taonani, ndidzalamulira, ndipo ndidzapeta nyumba ya Israele mwa amitundu onse, monga apeta tirigu m'lichero; koma silidzagwa pansi diso, ndi limodzi lonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Ai, ndidzalamula, ndipo ndidzagwedeza Aisraele uku ndi uku pakati pa mitundu yonse ya anthu monga momwe amagwedezera sefa uku ndi uku, popanda kamwala nkamodzi komwe kogwa pansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “Pakuti ndidzalamula, ndipo ndidzagwedeza nyumba ya Israeli pakati pa mitundu yonse ya anthu monga momwe amasefera ufa mʼsefa, koma palibe nʼkamwala kamodzi komwe kamene kadzagwe pansi.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 9:9
14 Mawu Ofanana  

Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Yehova adzaomba tirigu wake, kuchokera madzi a nyanja, kufikira kumtsinje wa Ejipito, ndipo mudzakunkhidwa mmodzi, inu ana a Israele.


Tirigu wa mkate aperedwa; pakuti samampuntha osaleka; ngakhale kuyendetsapo njinga ya galeta wake, ngakhale kumphwanya ndi ziboda za akavalo ake sapera.


ndi mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira, umene ufikira m'khosi, kupeta mitundu ya anthu ndi chopetera cha chionongeko; ndi chapakamwa chalakwitsa, chidzakhala m'nsagwada za anthu.


Ngati malembawa achoka pamaso panga, ati Yehova, pamenepo mbeunso ya Israele idzaleka kukhala mtundu pamaso panga kunthawi zonse.


Usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; pakuti Ine ndili ndi iwe; pakuti Ine ndidzathetsa mitundu yonse kumene ndinakuingitsirako iwe, koma sindidzakuthetsa iwe; koma ndidzakulangiza ndi chiweruziro, ndipo sindidzakusiya konse wosalangidwa.


Pa Elamu ndidzatengera mphepo zinai kumbali zinai za mlengalenga, ndidzamwaza iwo kumphepo zonsezo; ndipo sikudzakhala mtundu kumene opirikitsidwa a Elamu sadzafikako.


ndipo ndidzasankhula mwa inu opanduka ndi ondilakwira, ndidzawatulutsa m'dziko logoneramo iwo; koma sadzalowa m'dziko la Israele; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


ndipo ndinawabalalitsa mwa amitundu, namwazika m'maiko monga mwa njira yao; ndi monga mwa machitidwe ao ndinawaweruza.


Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, popeza ndinalola atengedwe ndende kunka kwa amitundu, koma ndinawasonkhanitsanso akhale m'dziko lao, osasiyakonso mmodzi yense wa iwowa.


Chifukwa chake atate adzadya ana pakati pako, ndi ana adzadya atate ao; ndipo ndidzachita maweruzo mwa iwe, ndi akutsala onse ndidzawabalalitsa kumphepo zonse.


Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa kumphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata.


Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi mizinda yanu idzakhala bwinja.


Simoni, Simoni, taona, Satana anafunsa akutengeni kuti akupeteni ngati tirigu;


Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu ina, imene simunaidziwe, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa